Apolisi m’boma la Zomba amanga njonda ina kamba kopezeka ndi ma simukadi a lamya okwana 99 omwe njondayi imafuna kuti ilowetse mundende ya Zomba.
Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali, mkuluyi yemwe dzina lake ndi Tamani Sulumba wazaka 35 zakubadwa, anapita kundendeyi kuti akaone mzake yemwe adanjatidwa pamlandu wakuba.
A Sulumba ananyamula botolo la mafuta odzola lomwe iwo amati akamupatse mzawoyo kuti azikadzola. Apa woyang’anira ndende atafufuza chomwe chinali mkatimo anapezapo ma kadi 99 omwe awili ndi a Tnm pomwe 97 ndi a Airtel.
Izi zinapangitsa woyang’anira ndendeyo kuyifusa mafunso njondayo chifukwa chomwe inatengera makadiwo apa njondayi inalephera kuyankha.
Apa sanachedwe koma kunjata njondayo kuti ikafotokoze bwino bwino cholinga chomwe inali kuchitira izi. Pakadali pano mkuluyo akusungidwa mchitokosi cha apolisi ku zomba komweko.
A Sulumba amachokera m’mudzi mwa Masanjala Mfumu yaikulu Mpama m’boma la Chiradzulu ndipo akuyembekezeka kuyankha mulandu olowetsa katundu osaloredwa mundende.
Wolemba: Ben Bongololo