Zotsatira za NGC zayamba kufika: Mutharika wauza Msonda kuti atha kubwelera ku PP


DPP president Peter Mutharika

Mwina anakadziwa a Ken Msonda sanakapita ku nkumano wa akuluakulu a chipani cha DPP (NGC) omwe ukuchitikira ku Mangochi chifukwa mtsogoleri wachipanichi a Peter Mutharika, wawasambitsa chokweza, kuwatsukuluza mpaka kuwauza kuti ngati samakonda chipanichi abwelere ku PP.

Mu nkhani yathu m’mawa wa lero tinafotokoza kuti a Msonda omwe m’mbuyomu amaonetsa kuti ali mbali yomwe ikutsutsana ndi ulamuliro wa a Mutharika ku chipanichi, ali nawo ku nkumano wa National Governing Council omwe ukuchitiki ku hotela ya Sunbird Nkopola m’boma la Mangochi.

Koma poyankhula ku nkumanowu, a Mutharika anadzudzula mamembala ena omwe akuti ndigwero la mpungwepungwe omwe ukuchitika ku chipanichi ndipo sanapsatire mawu pa bambo Msonda koma kuwauza kuti atha kuwona nsana wa njira.

Mtsogoleri wa DPP-yu wati ndizodandaulitsa kuti a Msonda ndi m’modzi mwa mamembala a chipanichi omwe akangalika kwambiri kunyoza utsogoleri wawo chonsecho iwowo simembala weniweni wa DPP, koma analowa chipanichi kuti adzasokoneze.

“Ena mwainu makamaka bambo Nsonda mwakhala mukunyoza kwambiri, komaso sinu membala wa chipani chino. Munalowa chipani chino kuchokera ku PP (People’s Party) ndipo munabwera kudzaononga chipani chino.

“Ndikufuna ndikupempheni kuti ngati simumakonda chipani chino, mubwelere ku PP chomwe ndi chipani chanu, osawononga chipani chino. Inu kunalibe nthawi imene Joyce Banda amatithira utsi othetsa misonzi,” wakalipa Mutharika.

Mbali inayi kanema wina yemwe akuzungulira m’masamba nchezo akusonyeza a Msonda akupepesa ndipo anayankhula zokometsera a Mutharika mpaka kufika ponena kuti akuyenera ayimeso pa komveshoni ya chipanichi.

Iwo ati mlandu omwe unalipo omwe iwo ndi anthu ena anakamang’ara kuletsa a Mutharika kudzaimaso pa komveshoni yomwe ikuyembekezeka kuchitika chaka chino, anawuthetsa kutelo kuti a Mutharika ndiwoloredwa kutelo.

“Zimene tinapanga ifeyo atatu, tinamuuza loya kuti tathetsa mlandu. Lero kulibe mlandu, muyima chifukwa ife tinathetsa mlandu, muyimaso. Ine mpakana lero ndi ali ndisanasankhe kandideti chifukwa timadikira inuyo,” watelo Msonda.