Kwatuluka zithunzi zam’nanu pa masamba anchezo zothyakulidwa muphika otchedwa Photolab; komatu zithunzi zina ukaziona munthu ukumapukusa mutu kuli kusamvetsa kuti nzanga uja ndi uyuyu? Atayela komaso kutchena mochititsa kaso.
Photolab ndi apulikeshoni (application) ya mufuni yomwe anthu amayigwiritsa ntchito kukongoletsa zithunzi ndipo ili ndi zitakataka zamakono zomwe zadzetsa chimwemwe chodzadza tsaya kwa ogwiritsa ntchitowo.
Zina mwa zinthu zomwe zapangitsa kuti anthu agwe m’chikondi ndi apulikeshoniyi ndi monga kuthekera koyeretsa munthu, kukongoletsa komanso kuchotsa ziphuphu zonse pakhungu la munthu munchithunzi chothyakulidwacho.
Kupatula apo ogwilitsa ntchito apulikeshoniyi akumakhalanso ndi mwayi osintha zovala za munthu munchithunzi chomwe chikuthyakulidwacho komaso kuonjezera apo, pali tizinthu tina towonjezera mudyo wa chithunzicho monga wotchi (watch) ya pa mkono ndiso magalasi a m’maso.
Kubwera kwa apulikeshoniyi m’dziko muno kwadzetsa chifwilimbwiti cha zithunzi m’masamba a mchezo kaamba koti ambiri sakufuna kutsalira koma kuzijudura mothetsa mankhalu.
Zina mwa zithunzi zomwe zadya wani pa tsamba la fesibuku zophikidwa ndi Photolab ndi zakatswiri ochita zisudzo mdziko muno Tame Yusuf Mwawa amene anatchuka ndi dzina loti Ching’aning’ani.
Mchithunzichi, Ching’aning’ani watchena suti, wotchi, magalasi zonse zapamwamba ndipo akuwoneka wanthete, mwachikoka zedi komaso ngati khumutcha ndipo chithunzichi chagawidwa kwambiri komaso chalandira ndemanga zochuluka zedi.
“M’bale wanga izizi akulozapo chabe ena azitengera ngati walemeradi . angongole akuvuta kwambiri ndipo samva kupepesa…komanso umangidwa a MP akudela kwako sakuonera kukondwa…….Utenga nazo matenda izi Ching’aning’ani,” watelo Kondwani Kachamba Ngwira kwinaku atayika chithunzi cha Ching’aning’ani.
Pakadali pano anthu ochuluka akuyamikira apulikeshoniyi kuti ndiya bwino ngakhale kuti ena ati iliso ndikuyipa.
“Ubwino wake ndi oti ukamaziona zachimidzi akamapanga anzako koma ukumasilira mene akuonekela ndiposo akumapangawo akumakhala anthu omwe iweyo kuzifanizila ndiwowo ukhoza kukhala wachimidzi ndiwe kapena okongolaso pachione ndiwowo. And photo lab ija ili ngati mene amakhalira ma application ena onsewa omwe ali ndi ma effect , filter etc. Kungoti iyiyi ndiija yokokomeza yomubebesa munthu wadzidziwa
“Kuipa kwake ndikuja koti ukhoza kubeledwa ndalama kutumiza thilansipoti kwa munthu oti kukumana naye maso ndi maso pepa. Zikungofunika kulimba mtima kuvomeleza kuti ndi ma effects chabe sikuti munthuyo amaoneka choncho. Ndipo kuipa kwina ndikotii aliyense ndikuti aliyense angopanga nawo zija zoti palipose kufikaso pobowa. Koma nanga tita zabwela basi ndife a malawi tikapuma kumwamba,” watelo munthu wina pa fesibuku.
Malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza pa intaneti, apulikeshoni ya Photolab inapangidwa ndi kampani ya Linerock Investments LTD, yochokera ku San Fransisco, mdziko la United States.