Mtolankhani wa wailesi ya Ufulu ku Chikwawa wamenyedwa ndi anthu omwe sakudziwika patangotha masiku angapo ataulutsa nkhani ya mnyamata wina yemwe akudwala nthenda ya COVID-19.
Kumayambiliro asabata ino wailesi ya Ufulu inaulutsa nkhani yomwe mtolankhani wawoyu Macmillan Mozeyo amayankhula ndi mnyamata yemwe boma linalengeza kuti wapezeka ndikachilombo ka Corona.
Wachinyamatayu Ismael Maluwa yemwe amakhala kwa Ngabu anauza Mozeyo kuti akuona kuti padachitika chinyengo pakumuulutsa kuti iye wapezeka ndi kachilombo ka Corona sabata zingapo zapitazo ndipo anapempha kuti boma limuuze chilungamo chankhaniyi.
Potsatila nkhaniyi, anthu anayi omwe sakudziwika anagwira ndikuvulaza Mozeyo usiku wa lachitatu pafupi ndi nyumba yake m’boma lomwelo la Chikwawa.
Mtolankhaniyu wati anthuwa anamuuza kuti akumumenya kaamba kankhani yomwe analembayi ati ponena kuti Mozeyo waipitsa mbiri yaboma.
Anthuwa omwe sanagwidwe pakadali pano, adagwira ndikumumenya mtolankhaniyu pomwe amapita kunyumba kwake chamma 7 madzulo patsikuli ndipo anamuvulaza pachipumi kenaka anathawa onse.
Mozeyo analandira thandizo lachipatala ndipo pakadali pano nkhaniyi yakasiyidwa kwa apolisi a m’bomali omwe ati akhazikitsa kafukufuku osaka anthu omwe achita chipongwechi.
Pakadali pano bungwe loyang’anira atolankhani mdziko muno la MISA Malawi ladzudzula Mchitidwewu ndipo lati ndilokhumudwa kuti nkhani zakuzuzidwa kwa atolankhani zikupitilirabe mdziko muno.
Wapampando wa MISA Malawi a Teresa Ndanga mu mchikalata chomwe atulutsa lachinayi ati ndizokhumudwitsa kuti anthu sakulemekezabe ntchito zomwe atolankhani amakhala akugwira podziwitsa anthu zochitika zosiyanasiyana.
“Bungwe la MISA Malawi ndilodandaula kwambiri kaamba koti atolankhani akupitilirabe kuzuzidwa. Ndipo ndizokhumudwitsa kuti mpaka pano omwe achita izi sanadziwikebe ndipo izi zimabweretsa mantha pakati pa atolankhani ngakhaleso anthu ena.
“Ndiye tikufuna tinenetse apa kuti kukhala mtolankhani simulandu ndipo tikupempha aMalawi onse kuti ayambe kulemekeza atolankhani omwe malamulo adziko lino amawapatsa ufulu ogwira ntchito yawo.” Watelo Ndanga mumchikalata.
Bungwe la MISA Malawi lapemphaso apolisi a m’boma la Chikwawa kuti ayesetse kusaka ndikugwira nsanga anthu achitira chipongwe mtolankhaniyu ndipo lati anthuwa akagwidwa akalandire chilango monga mwamalamuloa dziko lino.