Kampani ya AstraZeneca yavomera kuti katemera wake wa Covid-19 atha kuyambitsa mavuto ena mthupi

Advertisement

A Malawi omwe anabayitsa katemera wa AstraZeneca pofuna kupewa mulili wa Covid19 ayamba kukhala mwa mantha pomwe kampani yomwe imapanga katemerayu yauza khothi kuti pali kuthekera kuti katemera wawoyu, nthawi zina, atha kuyambitsa zovuta zina mthupi mwa munthu.

Nkhaniyi ikubwera pomwe anthu okwana makumi asanu ndi m’modzi (51) anakasumira kampani ya AstraZeneca ponena kuti katemera wawoyu wawabweretsera mavuto osiyanasiyana mthupi mwawo.

Malingana ndi nyuzipepala ya The Daily Telegraph ya m’dziko la United Kingdom, m’modzi mwa odandaulawa ndi a Jamie Scott omwe akuti pano akukumana ndi mavuto ochuluka mthupi mwawo kutsatira kubayidwa katemera wa Covid-19 wa kampani ya AstraZeneca m’chaka cha 2021.

A Scott omwe ali ndi zaka 46, anauza nyuzipepala ya The Daily Telegraph kuti anakadziwa kuti katemerayu amabweretsa zovuta zosiyanasiyana mthupi la munthu, sanakalora kubayidwa.

Mkuluyu wati atabayidwa katemerayu ankaona chizumbazumba, ankava mutu kupweteka kwambiri, ankasaza kwambiri,  komaso sankakwanitsa kuyankhula ndipo anagonekedwa mchipatala ali chikomokere kwa masiku opitilira makumi atatu (30).

Kuyambira pomwe anthu anayamba kudandaula za mavuto omwe akukumana nawo akabayidwa katemerayu, kampani ya AstraZeneca yakhala ikutemetsa nkhwangwa pa mwala kuti katemera wawoyu samabweretsa vuto lili lonse pa matupi a anthu.

Koma posachedwapa, AstraZeneca yavomereza kuti m’nyengo  zina katemera wawo atha kubweretsa mavuto  ena mthupi la munthu.

Kudzera mu kalata yomwe inapeleka ku bwalo la milandu m’dzikolo, AstraZeneca yati izi sizikutanthauza kuti vuto lili lonse lomwe anthu omwe akudandaulawa anakumana nalo linayambitsidwa ndi katemerayu.

“Ndizovomerezeka kuti katemera wa AZ, nthawi zina, amayambitsa TTS (Thrombosis with Thrombocytopenia Syndrome), Njira yoyambitsa sikudziwika.

“Kupitilira apo, TTS imathanso kuchitika ngakhale palibe katemera wa AZ (kapena katemera aliyense). Zoyambitsa pazochitika zilizonse zitha kukhala nkhani yaumboni wa akatswiri,” inatelo kampani ya AstraZeneca m’mwezi wa February chaka chino.

Zadziwikaso kuti mkati mwa milandu 51 yomwe kampani ya AstraZeneca ikuyankha, ina inasumilidwa ndi abale a anthu omwe anamwalira atabayidwa katemera wa kampaniyi ndipo akuti anthu onse akufuna chipepeso chokwana £100 million yomwe ndi pafupifupi K217.6 billion.

Nyuzipepala ya The Daily Telegraph yalembaso kuti boma la UK mbuyomu linapeleka ndalama ya chipepeso kwa bambo Scott yokwana £120,000 yomwe ndi pafupifupi K262 miliyoni.

AstraZeneca anali m’modzi mwa a katemera omwe anthu amabayidwa m’dziko muno pofuna kuthana ndi matenda a Covid-19 ndipo nkhani iyi yadzetsa mantha pakati pa anthu omwe adabayidwa katemerayu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.