Kulekelera kudzivulazabe zipani pa masankho

Advertisement
Peter Mutharika

Akatswiri ozukuta bwino nkhani za ndale mdziko muno a Chimwemwe Tsitsi ndi a Victor Chipofya ati zipani zandale zikapitilira kutayiilira kuti zili ndi madela omwe amawati ndi amphamvu zililira kuutsi pa zotsatira za zisankho.

A Tsitsi ati zipani ziphunzire kuti pamene zili ndi dela lomwe kumachokera owatsatira ambiri sakuyenera kutayilira kuti mzachidziwikire kuti adzipambana pa masankho ponena kuti ndale zikusintha.

Akatswiri awiriwa ayankhula izi ndi wayilesi ya Zodiak lachitatu ku Blantyre pamene wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission MEC a Annabell Mtalimanja amalengeza zotsatira za masankho achibweleza amene anachitika ku madela a makhansala a Mwasa ndi Chilaweni.

Katswiriyu wati chipani cha Malawi Congress (MCP) chakatenga mpando wa khansala wa Mwasa wadi pamene poyamba yemwe ankayimira adali wa United Democratic Front UDF ndipo mzosabisa kuti chipani cha UDF kumeneku mkuchipinda kwawo ndipo awonjezera kuti zipani zonse zikuyenera kuika ndondomeko zakuthwa m’madela onse ponena kuti zili ndi kuthekera kopambana ku dela lomwe ena amati kuli mphamvu zawo.

A Victor Chipofya ati mkofunika kuti onse opikisana nawo pa ndale adziyika umoyo wa anthu patsogolo ponena kuti ndale za dzipani zili ndi kuthekera kosadalilika masiku ano ndipo apempha kuti opikisana nawo komanso zipani zidzitsata malamulo mcholinga chochepetsa madando a part zotsatira za masankho.

Wapampando wa bungwe la MEC analengeza kuti a Steward Mwase a chipani cha MCP ndi amene anapambana ku dela la Mwasa m’boma la Mangochi atapeza ma voti 1,073 kupitilira anthu ena anayi omwe amapikisana nawo, pamene a Maxwell Chipiliro Phiri oyima pawokha ndi amene apambana ku dela la Chilaweni m’boma la Blantyre atapeza ma voti okwana 1882 kuposa anzawo onse asanu ndi atatu omwe amapikisana nawo.

Masankhowa adachitika kutsatira imfa ya omwe anali ma khansala a m’maderawa.

Advertisement