A Phungu ena a MCP amagawa soya pieces ndi ndalama pa malo olembetsera – Mkandawire 

Advertisement
Voter Registration

M’modzi mwa akuluakulu a gulu la Chisankho Watch omwe amayang’anira ntchito za chisankho m’dziko muno, wauza atolankhani mu mzinda wa Lilongwe kuti kalembera wa gawo la chitatu unakumananso ndi mavuto akulu monga ziphuphu.

Iwo anati a phungu ena a chipani cholamula cha Malawi Congress amagawa ndalama komanso soya pieces kwa anthu omwe amalembetsa komanso omwe amagwira ntchito yolembetsayi.

Malinga ndi a Mkandawire, Phungu wina wa wa MCP pa malo ena olembetsera a Nyamithuthu m’boma la Nsanje, anagawa ndalama zokwana K10,000 kwa omwe amagwira ntchito ya kalemberayu (MEC staff).

Iwo anati izi ndikuphwanya malamulo a zipani omwe anayikidwa mu chaka cha 2018 (Political Parties Act (2018).

A Mkandawire anauzanso atolankhani kuti khalidwe loyipali linachitikaso ku Lilongwe ku Likuni komwe phungu winanso wa MCP anapita pa malo a kalembera pomwe anakagawa ndalama komanso Soya pieces kwa anthu omwe amalembetsa.

” Phunguyu analonjezanso anthu omwe amalembetsa pamalopo kuti adzapatsidwa ngongole za NEEF ngati angavotere MCP chaka cha mawa ndipo tsiku lotsatira anakagawira anthu olembetsa ma K5,000,” iwo anatero.

A Mkandawire anafotokozanso pa mkumanowu kuti, Ku Mtandire-Msiliza komanso ku Lilongwe Demera Phungu winanso wa MCP anakagawira anthu ma K2,000, 

ma K1,000 komanso soya pieces kwa olembetsa.

A Mkandawire anati zomwe zinachitikazi ndi zotsutsana ndi malamulo a dziko lino.