Bushiri wagawa chimanga ku mawanja okhudzidwa ndi madzi osefukira ku Mangochi

Advertisement

Pomwe miyanda miyanda ya anthu omwe amakhala mphepete mwa nyanja ya dziko lino akhudzidwa ndi vuto lakusefukira kwa madzi, mtsogoleri wampingo wa Enlightened Christian Gathering, mneneri Shepherd Bushiri wagawa chimanga ku mawanja okhudzidwa oposa 200 ku Mangochi.

Anthu ambiri omwe amakhala mphepete mwa nyanja ya Malawi, asamukira kaye m’madera akumtunda kamba kakusefukira kwa nyanjayi zomwe zapangitsa kuti ambiri mwa iwo asowe chakudya ndi malo okhala.

Potsatira vutoli mneneri Bushiri yemwe aku gawa kale chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala, Lolemba pa 22 April, 2024, anathamangira kudera la mfumu yaikulu Nankumba ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi komwe vutoli lakura.

A Kusakala kugawa chimanga m’malo mwa a Bushiri.

Uku Bushiri wagawa chimanga kwa mawanja opitilira 200 omwe anathawa m’nyumba zawo kamba ka kusefukira kwa madziku ndipo akukhala m’malo ongoyembekezera otchedwa Nankhwali ndi Sungo.

Kudzera mwa owayankhulira awo a Aubrey Kusakala, mneneri Bushiri wati wa gawa chakudyachi kamba koti akuzindikira zovuta zomwe anthu omwe ali m’mavuto ngati awa amakumana nazo.

A Kusakala ati aka ndi kachitatu kugawa chimanga m’boma la Mangochi ndipo ati mneneri Bushiri satopa ndikuthandiza anthu omwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana mdziko muno.

Poyankhula za thandizoli, mfumu yaikulu Chiwalo, yathokhoza mneneri Bushiri kamba ka thandizoli ndipo yamema anthu akufuna kwabwino komaso makampani kuti atengele chitsanzo pa zomwe wachita mneneriyu.

“Ife tikufuna tithokoze kwambiri prophet Bushiri kamba koti sakutopa kutithandiza ndipo ndikanakonda kuti anthu enaso atengere chitsanzo pa ntchito ya bwinoyi chifukwa omwe agwa m’mavuto ngati awa alipo ochuluka zedi mdziko muno,” yatelo mfumu Chiwalo.

M’mwezi wa February chaka chino, Bushiri anakhazikitsa ntchito yogawa chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala ndipo kufika pano, anthu oposa 700,000 ndi omwe apindura mundondomekoyi.

Ena mwa maboma omwe apindura ndi ndondomekoyi ndi monga; Karonga, Nkhotakota, mzinda wa Mzuzu, Nkhatabay, Ntcheu Lilongwe, Nsanje, Mulanje, Thyolo ndi Zomba.

Advertisement