Tsopano nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo yati kuyambira mawa pa 1 February mvula ikhala ikugwa m’dziko muno patapita pafupifupi sabata ndi masiku kopanda mvula maka m’madera am’chigawo chapakati komanso kum’mwera kwa dziko lino.
Malingana ndi mneneri ku nthambiyi a Yobu Kachiwanda, ati mvula ikhala mwezi onse uno wa February.
Kachiwanda wati ngakhale kuti mvulayi ikhala ikugwa m’mwezi umenewu koma kuzikhalanso kopanda mvula masiku ena.
Alimi osiyanasiyana anali ndi chikaiko kuti chaka chino sakolola mokwanira kamba koti kusowa kwa mvulaku kudakapangitsa kuti mbewu zawo zisachite bwino