Dziko la Israel likufuna a Malawi okwana 100,000


Dziko la Israel lati likufuna a Malawi okwana 100,000 kuti akagwire ntchito zosiyanasiyana ku Israel.

Izi zayankhulidwa lero pamene  nduna  ya zachuma mu dziko la  Israel,  Nir Barakt,  anali ndi mkumano ndi mlembi wamkulu mu unduwa wa zachuma mu dziko lino Dr Betchani Tchereni.

A Barakt atsimikizira kuti mwai wa ntchito ulipo wambiri dziko la Israel maka minda ndi zomangamanga.

Ndunayi inafusa a Tchereni kuti pangatenge nthawi yochuluka bwanji  kuti mzika za dziko lino zokwana 10,000 zipite dzikolo kukagwira ntchito.

Mukuyankha kwawo, a Tchereni anatsimikizira ndunayi kuti kwa sabata limodzi izi ndi zitheka ngati dziko la Israel tingathandizire anthuwa mayendwe.

Mthumwiyi itatha mkumanowu inatsimikira a malawi kuti uwu ndi mwai kwaukulu kwa achinyamata a dziko lino kukagwira ntchito Ku Israel.

Wolemba: Peter Mavuto

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.