…Bullets yakanika kuzemba pa Mazembe
Zikakhala nyerere zikuti ndi chifukwa kunalibe ma ref ogulitsa, eni ake a Bullets ati bola anafikako ku CAF. Koma lero pa 30 Sepitemba ulendo wa Bullets watha basi. Mazembe ya Joseph Kamwendo yachita chobaya. Kulasa mu nthiti akazembe a dziko lino anga ndi a gwape.
Pa masewero achiwiri amene anachitika mu chikho cha ma kalabu a mu Africa, timu ya ku Congo ya TP Mazembe yapitiriza pamene inasiyira itabwera kuno kuzakumana ndi Bullets. Koma mmalo mongopambana ndi chigoli chimodzi monga anachitira pa Bingu, Mazembe pa kwawo yaphunzitsa Bullets mpira. Kuonetsetsa kuti akatswiri a ligi ya ku Malawi’wa, akamabwera akhale ali zyoli.
Chipongwe cha Mazembe chinayamba patangotha mphindi zinayi. Timuyi inamwetsa chigoli, kutumiza uthenga kuti lero pali ndombolo pano. Ngati a Bullets anali ndi chikayiko kuti mwina nkuphulapo kanthu, a Mazembe anathira mpholopolo wina patatha mphindi khumi ndi imodzi basi (11) kuti masewerowa, ku Lubumbashi kokha, akhale 2 kwa du.
Panalibe kupumitsa timu ya Bullets lero chifukwa a Mazembe, mu mphindi makumi awiri (20) iwo anakhomelamo chigoli chachitatu mu ukonde wa Bullets. Ndiye anatutumuka mphunzitsi wa maule a Callisto Pasuwa ndikuyambapo kubakashabakasha osewera. Anatulutsa atatu kuti mwina abise manyazi. Koma akanadziwa akanangozisiya kapena kupanga za Noma zonyanyala basi.
A Mazembe anathira mpholopolo yachinayi kupangitsa kuti Bullets ikhale ngati yachidima, ngati yosaudziwa mpira ndi komwe. Mmene oyimbira amaimba khelere kuti anthu akapumulire ndiye kuti pa zigoli zokha za ku Lubumbashi zili zinayi kwa chete. Kuphatikiza ndi za kumudzi komkuno, zisanu za Mazembe ndipo palibe kwa Maule.
Chigawo chachiwiri zinaonetsa kusintha, anyamata a Bullets anazitolera. Koma ndiye kuimba chiminingo njobvu zitaononga kale. Ngakhale sanagoletsedwe choonjezera, koma iwo sanapaonenso. 5 kwa du basi. Kwa Bullets kwatha.