Coronavirus: Boma labwezeretsa ziletso

Advertisement

Pomwe chiwerengero cha anthu omwe akupezeka ndikachilombo ka corona chayambilaso kukwera, boma labwezeretsa zina mwaziletso zomwe pakatipa zinasiya kugwira ntchito.

Izi zadziwika lachitatu masana pomwe nduna yazaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda omweso ndi mmodzi mwa akuluakulu akomiti yamtsogoleri wa dziko yoyang’anira ntchito yolimbana ndi mlili wa covid-19, amayankhula pansonkhano wa atolonkhani ku Lilongwe.

Malingana ndi a Kandodo Chiponda, ndizokhumudwitsa kuti chiwerengero cha odwala komaso omwalira ndi matenda a covid-19 m’dziko muno chikukwera pomwe posachedwapa chinatsika kwambiri.

Iwo ati potsatila kukweraku, ndikofunika kuti aliyese atenge mbali pofuna kugonjetsa mliliwu ndipo ati ndi chifukwa chake boma mogwirizana ndi komiti yotsogolera ntchito yolimbana ndi mliliwu yabweretsaso zina mwa ziletsozi.

Zina mwaziletsozi ndimonga kuchepetsedwa kwa chiwerengero cha anthu opezeka mmiyambo ya maliro ndipo apa ndunayi yati mnyumba yamaliro muzikhala anthu osapitilira 10 komaso maliro aliwose aziikidwa pasanadutse masiku awiri.

Ndunayi yatiso mimkumano kuphatikizapo mapemphero ndi maukwati pazikhala anthu osaposera 50 ngati akupangira mnyumba ndipo ngati ndipanja anthu asamapitilire 100 ndipo pamaukwati a Chiponda ati ukwati uzichitika mosapitilira ola limodzi.

A Chiponda ayimitsa kaye misonkhano ya ndale ndipo alamulaso kuti mpira uzimenyedwa popanda owonelera pomwe malo omwera mowa awalamula kuti azitsekulidwa 2 koloko masana ndikutsekedwa 10 koloko usiku.

Kuonjezera apo,ndunayi yalamulaso kuti ma minibasi apitilire kutenga anthu ochepa pomwe ochita malonda mmisika awauza kuti azionetsetsa kuti pazikhala mpata waukulu pakati paogula ndi ogulitsa.

Ngakhale zilichonchi, a Kandodo Chiponda ati masukulu akhalabe otsekula komaso ati anthu ofuna kupita maiko akunja aziloledwa kutelo koma ati anthu omwe azichokela mmaiko omwe nthendayi yavuta azikasungidwa kaye kumalo kwaokha kwamasiku 14.

Kuchokera mwezi wa June chaka chino kufika pano, anthu oposera 3000 ndiomwe apezeka ndikachilombo ka corona pomwe anthu oposera 100 ndiomwe agonekedwa mzipatala komaso anthu oposera 60 ndi omwe amwalira ndimatendawa

Advertisement