Tikulemba anthu opuma pa ntchito kuti tibwezeretse mwambo mu boma – Chakwera

Advertisement

Pulezidenti wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati boma la mgwirizano wa Tonse likulembanso anthu opuma pa ntchito kuti athandizire kubweretsa mwambo pogwira ntchito za boma.

Iwo ananena izi ku nyumba ya malamulo pomwe amayankha funso lomwe phungu la dera la Nkhotakota North East anafunsa kuti chifukwa chiyani akumatero.

A Chakwera anati ndizosamveka kunena kuti boma silikupeleka mpata kwa achinyamata kuti atumikire dziko lino poti ndi anthu ochepa chabe omwe awayitanaso kuti akagwire ntchito.

Atafunsidwa ndi phungu wa dera la Balaka East kuti boma layika njira zanji zothandizira anthu omwe akhudzidwa ndi njala yodza kamba ka kusefukira kwa madzi monga ku Balaka, a pulezidenti anati boma layika kale ndondomeko zothandidzira anthuwa ndipo akhala akulandila zakudya kuyambira mwezi wa mawa ndipo ena akhala akuthandidzika kudzera mu ndondomeko ya mtukula pakhomo.

Boma la mgwilizano wa Tonse pa nthawi yokopa anthu idalonjeza achinyamata kuti azakonza njira zoti achinyamata miliyoni imodzi pa chaka chilichonse adzilembedwa ntchito, zomwe anthu ambiri akufunsa kuti sakuwonapo kuthekera kuti zipheledzera.

Advertisement