Ma Jaji awiriwa achotseni si a chinyengo – Mvalo

Advertisement
Malawi Justice Minister

Pomwe nkhani ya katangale pakati pa oweruza milandu komaso oyimilira anthu pa milandu ikupitilira, nduna ya zachilungamo Titus Mvalo, wayikira kumbuyo oweruza milandu awiri omwe akuganizilidwa kuti amapanga katangale.

Poyikira mlomo pa gulu lina la pa WhatsApp za mndandanda wa oweruza milandu omwe akuganizilidwa kuti akhala akupanga katangale, Mvalo wati oweruza milandu Nyakaunda Kamanga ndi Ivy Kamanga, achotsedwe pa ndandandawu ponena kuti awiriwa za katangale ndi mphaka ndi khoswe.

A Mvalo ati; “Ndawona pano mndandanda wa majaji omwe akuganiziridwa kuti ndi a katangale omwe ndikuphatikizapo amayi awiri oweruza milandu ku Khoti Lalikulu la Apilo, Nyakaunda Kamanga ndi Ivy Kamanga. Ndikupempha kuti awa achotsedwe pamndandandawo. Nsikulakwitsa kuwaphatikiza pamndandanda wotere chifukwa iwo samachita katangale, ndipo ngakhale woululayo, Kamangila, adawatchula kuti si achinyengo.”

Masabata awiri apitawa woyimilira anthu pa milandu Alexious Kamangila adawulura kuti oweruza milandu komaso oyimilira anthu pa milandu ambiri ndi a madyera mphoto. Izi zapangitsa magulu ochuluka ayitanitse kafukufuku ku mabwalo a milandu kuti onse omwe akukhudzidwa awone chidameta nkhanga mpala.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.