Msonkhano waukulu wa MCP: Zikhale, Chithyola amwaza K76.5 miliyoni pogula mavoti

Advertisement
Simplex Chithyola banda

Sin’dazione adachezera kuziona! 2025 akusunthira chifupi, a Malawi yembekezani kuona malodza: Pomwe inu mukusowa ka K500 kogulira mchere, nduna zanu ziwiri zagula mavoti a ku konveshoni ya MCP ndi K76.5 miliyoni. Kuli kanthu kokanthula nchala, ali ndi mwana agwiritsa!

Malingana ndi zomwe yalemba nyuzipepala ya Nation ya Lachisanu, nduna ya zachitetezo a Ken Zikhale Ng’oma komaso nduna ya za chuma a Simplex Chithyola Banda ndi omwe awonetsa kuti olamura boma samatuwa.

Nyuzipepalayi yati Lachitatu sabata ino, nduna ziwirizi zinali mchigawo cha kumpoto komwe zamwaza ndalama za nkhani nkhani kwa ma membala 153 a chipani cha Malawi Congress omwe akuyenera kukavota pa konveshoni yomwe chipanichi ikhale nayo mwezi wamawa.

Richard Chimwendo Banda
Chimwendo akumwaza ma miliyoni pofuna mavoti.

Pankumanowu omwe unachitikira pa Nyachenda Motel munzinda wa Mzuzu, a Zikhale Ng’oma anapeleka K45.9 miliyoni zomwe zinapangitsa kuti mamembala a chipaniwo agawane K300,000 aliyese.

Naye Chithyola Banda sanafune kutsalira koma kuvumbulutsa K30.6 miliyoni, kupangitsa anthuwo kuti agawane aliyese K200,000. Izi zapangitsa kuti anthu onse 153 omwe anali pa mkumanowu apite kwawo akululutira pomwe angotola K500,000 aliyese.

Zikhale Ng’oma walonjeza kuti akakawina ku konveshoniko adzawapatsaso anthuwa ndalama zina ponena kuti, “ndilibe zambiri koma poti paja ndine nyama zikuluzikulu, aliyese alandira K300,000 koma mukakandivotera ndidzawonjezera. Ndine munthu amene ndimasunga lonjezo.”

Pomwe mamembala a chipaniwo amaona ngati angopatsidwa ndalama zokha basi, nduna ziwirizi zinawapatsaso zinthu zina za makaka a chipani monga nsalu, ma T-shirt, zipewa, ma ambulera, komaso kwa omwe anachokera kunja kwa nzinda wa Mzuzu, analipililidwa malo ogona komaso kugulilidwa zakudya.

Ku msonkhano wa ukulu wa MCP omwe ichitikire munzinda wa Lilongwe, a Zikhale Ng’oma akupikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi, pomwe a Chithyola Banda akupikisana nawo pa udindo wa mlembi wamkulu wa chipanichi.

Advertisement