Ulendo wa ku  Israel wasanduka ngati opita ku kanani

Advertisement
Malawi Youths

Achinyamata oposa 50 mwa omwe akuyenera kupita kukagwira ntchito ku minda mdziko la Israel ulendo wawo ukukumana ndi zokhoma ndipo lero  ati agona ku ma ofesi a bwana mkubwa wa boma la Lilongwe  kudikira kuti akawapelekeze  ku ma ofesi a boma ku City Centre mu mzindawu kukapitiliza chilinganizo cha m’bindikiro wawo.

Malinga ndi mtsogoleri wa gululi yemwe Malawi24 yayankhula naye a Dingiswayo Kumwenda  wati  ngakhale apolisi awabweza kuti achoke ku ma ofesi a boma ponena kuti zikalata za umboni palibe, a  Kumwenda ati zikalata zonse zilipo.

“Tinawawonetsa zikalata zathu koma anatiopseza kuti atithira utsi,” anatelo a Kumwenda.

Achinyamatawa ati tsogolo la zokambilana zomwe akhala akukhala nazo ndi a ku ma unduna  komanso ena okhudzidwa zokhudza kukagwira ntchito mdziko la Israel zikuoneka sizikuphula kanthu ndipo ati kudzela mu m’bindikiro wawo womwe akonza ku ma ofesi a boma uthandiza kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera alowelelepo mwa nsanga.

Achinyamata oposa 2,000 anamaliza kale ndondomeko za ulendo wawo ndipo akungodikira kunyamuka ngakhale nthawi ya zina mwa zikalata zawo monga za chipatala  zikhale zikupitilira kutha mphamvu chifukwa cha kuchedwa, boma linakhazikitsa ndondomeko yakuti ulendo wa ku Israel lidzipanga lokha.

Masiku a m’mbuyomu achinyamatawa anathamangitsana ndi apolisi uku akuthira utsi chifukwa cha ziwonetselo zomwe anati sizinatsate ndondomeko.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.