Musandilankhulitse Pambali – Chakwera 

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa  dziko lino Lazarus Chakwera wati sibwino kunamiza aMalawi kuti dziko likhonza kumangidwa popanda maziko ovuta komanso  a misozi, ndipo kulankhula motha mawu otere ndi chifukwa choti omwe adali m’boma m’mbuyomu adaba ndipo palibe akuwalondola nde akuwona kuti nzophweka kungomanga dziko mwachidule.

Polankhula pa mwambo okhazikitsa zipangizo za makono za ulimi ku BICC  mu mzinda wa Lilongwe a  Chakwera ati kulankhula konena kuti akanakhala ndi mpata otsogolera  dziko sakanakumana ndi mavuto monga cyclone Freddy, Gombe, covid19, ngongole za Katapila zomwe anatenga, kuchoka kwa mathandizo ndi zina ati nzofuna kungolakhulitsana udyo.

“Mungotikhululukira anthu ena asatilankhulitse pambali.

“Amalawi wina asakunamizeni chiloweleni m’boma takhala tikuyika maziko osiyanasiyana kuti mtsogolomu mudzakolore chuma cha nkhani nkhani nde tonse tinangoyenela kulimba mtima poti nthawi  yoyika maziko ndi kufesa imakhala nthawi ya msozi koma sikuti wina apeze mwayi onamiza amalawi kuti akanakhala iwowo bwezi yumanga maziko osamva nawo kuwawa zimenezo ndi zabodza,” atero a Chakwera.

A Chakwera ayankhula izi chifukwa posachedwapa mtsogoleri wa DPP a Peter Mutharika anati akanakhala akulamulira ndi iwo bwezi Malawi ali pabwino.

Mtsogoleri wa dzikoyu anawonjezera kuti nkhani ikhale yonena kuti dzikoli lufunika kukonza maka kudzera mu ulimi wobwezeletsa nthaka komanso osagwiritsa ntchito khasu koma makina amakono kuti zokolola zikhale  zambiri.

Zipangizo za ulimizi zabwera mu mgwirizano wa Pyxus Agriculture Malawi, Phillip Morris international kuti zithandize alimi pa ulimi wa malonda polima minda ikulu-kulu kuthamangitsana ndi madomphenya a  2063.

Advertisement