Watsekeledwa wina chifukwa chonyoza Chakwera pa WhatsApp

Advertisement
Malawi president Lazarus Chakwera

Inu amene mukumapeza mwayi otsukuluza mkamwa pa nkhani zokhudza mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera yambani kuyenda mosamala. Ayamba kunjata anthu kunja kuno ati chifukwa chonyoza a Chakwera.

A Sainani Nkhoma a ku Dowa akuyembekezeka kumva chigamulo chawo sabata la mawa pamene a bwalo apeza kuti mkuluyu anatsukuluza mkamwa pothilira ndemanga pa nkhani yokhudza a Chakwera.

Apolisi adati a Nkhoma adayankhula mwachikunja nkhani yokhudza a Chakwera pa gulu lina la pa WhatsApp limene iwo analipo lotchedwa Mponela Hotspot. Ndipo ati anthu ena adakawasumira ku polisi.

Iwo atafika pa bwalo, a bwalo awapeza olakwa ndipo ati chigamulo chibwera sabata la mawa. Mwa zina, a Nkhoma atha kugamulidwa kukagwira wa kalavula gaga kwa zaka zisanu ndi chimodzi (6) kapena kulipitsidwa chindapusa cha 6 miliyoni.

A Malawi ochuluka poonetsa kusakondwa ndi kukwera mitengo kwa zinthu komanso komwe dziko likulowera akumapita pa masamba a mchezo kukhuthula zakukhosi kwawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.