Chizungu chikucheka ma galajuweti amene – atero a UNIMA

Advertisement
Sunduzwayo-Madise

Zadziwika kuti ophunzira ambiri a mu sukulu za ukachenjede chingerezi chikumawapeta ndipo ambiri sakwanitsa kufotokoza komanso kulemba m’chizungu chomveka bwino.

Izi ndi malingana ndi otsatira kwa wachiwiri wa Chancellor ku sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi (UNIMA), Dr Sunduzwayo Madise yemwe wati kusowa kwa ukadaulo pa kaphunzitsidwe kamakono maka kuyambira ku m’mela mpoyamba kukuwonjezera  kuvutika kwa ana a sukulu za  ukanjede kulankhula chizungu chomveka.

Polankhula pa chiwonetselo cha ukadaulo pa maphunziro maka pa kuphunzitsa ndi kuphunzira omwe unachitika pa sukuluyi ku Zomba, a Madise anavomeleza kuti sukuluyi ili ndi ophunzira ena omwe  akumavutika kufotokoza zinthu kapena kudzifotokoza okha mu chiyankhulo cha chizungu.

A Madise ati, “Tazindikira kuti pali kuchepa kwa luso la kaphunzitsidwe, vuto si ana a msukulu za ukanjedezi vuto ndi chiyambi, kuyambira ngakhale msukulu za pulayimale zomwe zupangitsa kuti tikhale ndi ana ena amene akuvutika ndi chizungu.”

“What we have noted is that there is a gradual reduction in terms of skills. It’s not their fault, the problem is at the base, the primary school. So we get some students who find it difficult even to express themselves or write clearly in English,” anatelo a Madise mu chizungu.

Pofuna kuchepetsa chiwelengelo cha kusachita bwino kwa ana msukulu za pulayimale, boma lidakhazikitsa ndondomeko za ukadaulo ndi ukatswiri wamakono pa kaphunzitsidwe mu msukulu kudzera mu ndondomeko ya Building Education Foundation through Innovation and Technology (BEFIT).

Advertisement