Namondwe wa Freddy komanso mchitidwe okuba zichitsulo cha njanji ndi zina mwa zomwe zachedwetsa ntchito yokonzaso njanji ya makilomita 72 ya Limbe-Sandama.
Nduna yoyang’anira mayendwe komaso ntchito, Jocobo Hara, wati pakadali pano sizikudziwika nthawi yeniyeni imene ntchito yi idzamalizidwe chifukwa contilakitala sakugwira ntchitoyi.
A Hara anauluraso kuti namondwe anaononga milatho yambiri imene imalumikiza njanjiyi komaso anthu amene akuba kwambiri zitsulo za njanji mbali yomwe inamalizidwa kukonzedwa.
Iwo anati ndalama zokwana K10.4 biliyoni ndi zomwe zaikidwa pa ntchito yi ndipo milatho yakwana 29 ndi yomwe ikuyembekezedwa kukonzedwa kuchokera ku Limbe kukafika Ku Sandama.
Ntchitoyi inayamba mu chaka cha 2017 kutsatira kusefukira kwa madzi kumene kunachitika mu mchaka cha 2015 ndipo milatho yambiri idakokoloka imene imalumikiza njanjiyi.
Wolemba : Peter Mavuto