Pomwe bwalo ya Kamuzu ili chikalambire ku Blantyre, dera lomwe linatchuka kwambiri nthawi ya ziwonetsero m’chaka cha 2019, Nsundwe, lalandira mphoto ya bwalo lochitilapo masewero lomwe boma lalengeza kuti likufuna kumanga kudelali.
Nkhaniyi yadziwika pomwe khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yatulutsa chikalata chomemeza ma kampani omanga kuti yomwe ingachite mphumi igwire ntchito.
Chikalatachi chikusonyeza kuti ‘stadium’ ikunenedwayi ikamangidwa kwa Nsudwe mdera la mfumu yaikulu Kalolo mu mzinda wa Lilongwe ndipo zikuoneka kuti ntchitoyi ikuyenera kuyamba chaka cha mawa.
“Khonsolo ya Lilongwe mothandizidwa ndi unduna wa maboma ang’ono, mgwirizano ndi chikhalidwe ikufuna kupereka malipiro oyenera pomanga bwalo la masewera ndi ntchito zina zakunja ku Nsundwe ku dera la mfumu yaikulu Kalolo m’boma la Lilongwe.
“Wapampando wa komiti yowona za kagulitsidwe ka katundu ku khonsolo ya Lilongwe akuitana anthu omwe ali ndi chidwi chogwira ntchitoyi, omwe ali mgulu la ‘Unlimited category’ (Building and Civil) ku National Construction Industry Council (NCIC) yaku Malawi, ku ntchito yomanga bwalo la masewera ndi ntchito zina zakunja kwa Nsundwe kwa T/A Kalolo m’boma la Lilongwe,” yatelo mbali ina ya chikalatachi.
Malingana ndi chikalatachi, kutsatsa ntchitoyi kuchitika motsatira ndondomeko za ma ‘tender’ zomwe zili mu Public Procurement and Disposal Act ya 2017 ndi Public Procurement Regulations ya 2020 ya boma la Malawi ndipo ndi onse ofuna kuchokera kumayiko oyenerera ndiololedwa.
Chikalatachi chatiso onse omwe ali ndi chidwi chofuna kugwira ntchitoyi atha kupeza zambiri ku khonsolo ya Lilongwe.
Pakadali pano, anthu akuyankhula zosiyanasiyana makamaka pa masamba a mchezo ndipo ena akuganizira kuti iyi ndi mphoto ku dera la kwa Nsundwe pa zomwe linachita m’mbuyomu.
“Izi ndi zabodza mwamtheradi. Apule chonde siyani misala imeneyi. Stadium ku Nsundwe pomwe tili kale ndi ma stadium atatu ku Lilongwe ndipo tikukanika kuwasamalira. Kamuzu Stadium yawonongeka, Mzuzu ilibe stadium yomangidwa bwino.
“Nsundwe ndi malo ochitira malonda chabe osati tawuni. Mwina ngati mukufuna kuwalipira chifukwa chophwanya malamulo, amangileni chinthu china, kaya ndi sukulu yaukachenjede kapena chipatala,” watelo Chatinkha Chidzanja Nkhoma pa fesibuku.
Dera la Nsundwe linatchuka kwambiri kutsatira zipolowe zomwe zinachitika chaka cha 2019 pomwe anthu akudelari anatseka mseu waukulu pofuna kuletsa magalimoto a yemwe anali mtsogoleri wa dziko nthawi imeneyo a Peter Mutharika kulowa munzindawu kukachititsa msonkhano wachitukuko.
Pofuna kubweretsa bata, apolisi adalowelerapo ndipo adawombera utsi wokhetsa misozi zomwe zinakwiyitsa anthuwa ndipo anagenda ndikupheratu wa polisi wina, malemu Usumani Imedi yemwe ankachokera m’boma la Mangochi.