Sindinabe feteleza, sindinalande wa polisi mfuti – oyendetsa thilaki Grey Chisinga wakanitsitsa

Advertisement
Firearm belonging to Malawi Police

..wadzudzula a polisi ya Kanengo pomunena kuti anasiya upolisi kuti adziba

Shoveli wa thilaki yemwe akuzemba unyolo, Grey Chisinga, wakanitsitsa kuti iye anaba ndikugulitsa feteleza yemwe adanyamula komanso wati sanalande wa polisi mfuti koma kuti wapolisiyo anayisiya mfutiyo pansi zomwe zinamupatsa mwayi kuti ayitenge ndikuombera m’mwamba.

Apolisi munzinda wa Lilongwe akusaka a Chisinga powaganizira kuti anaba ndikugulitsa matumba a nkhani nkhani a feteleza yemwe ananyamula munzinda wa Blantyre ndipo amayenera kukamusiya ku Lilongwe.

Kupatula apo, mkuluyu akuganizilidwaso kuti analanda wapolisi mfuti yomwe anagwilitsa ntchito powombera m’mwamba pa tsiku lomwe apolisi ankafuna kumumanga mkatikati mwa sabata yatha.

Koma a Chisinga omwe mpaka pano sakudziwika komwe ali, ayankhula ndi mzawo wina kudzera mu kilipi ya mawu ya pa WhatsApp (voice note) yomwe pano anthu akugawana m’masamba anchezo ochuluka, ndipo afotokoza tchutchu zomwe zinachitika.

Iwo ati sanabe fetelezayo monga momwe zikuvekera, koma ati munthu amene amawatsogolera ndi yemwe anawalamura kuti akatsitse fetelezayo ku malo ena omwe sanawatchule bwino bwino koma ati ndi ku Lunzu m’boma la Blantyre.

A Chisinga anauza mzawo yemwe amayankhula nayeyo yemwe amutchula kuti Thom kuti izi zitachitika, anakafotokoza ku polisi ya Kanengo munzinda wa Lilongwe ngakhale kuti apolisiwo samakhutitsidwa ndipo ankafuna kumumanga.

“Panali ejenti yemwe ndinapatsidwa kuti ndiyende naye kukatenga feteleza ku Optichem, kukatsitsa ku Lilongwe. Nde patsikuli tili pa Kameza kuti tizipita ku Lilongwe, ejentiyu anandiuza kuti zasintha katundu titsitsa ku Blantyre konkuno ndipo anandiuza kuti bwana anga awapatsa ndalama zawo zonse ngakhale kuti thilakiyi siipita ku Lilongwe ndi fetelezayo, ine osadziwa kuti pakuchitika china chake.

“Katundu anakatsika pena pake ku Lunzu ndinawauzaso apolisiwo. Nde ndi munthu yo tinatengana kubwera ku Lilongwe kudzasainutsa kuti katundu wayenda chonchi. Titafika ku Kanengo ananditsazika kuti akukasayinitsa kenaka anabwera. Nditamufusa ndalama ya bwana anga (transport fee) anandiuza kuti akukatenga ku banki, omwewo sanabweleleso, kuyimba foni yake siikupezeka mpaka pano,” atelo a Chisinga.

Iwo ati anayesa kuthandiza apolisi pa momwe angafufuzire nkhaniyi koma sadawamvere ndipo anenetsa kuti sakadzipeleka ku polisi pokhapokha apolisi afufuze bwino bwino kufikira chilungamo chidziwike kuti iwo sanabe fetelezayo.

“Sindingalore ndikakhale kundende pa zinthu zoti sindinachite, afufuze kaye bwino nkhaniyo. Kodi ineyo ndikanakhala kuti ndaba, bwezi ndili ku Malawi kuno? Feteleza ameneyoyo its around K40 to K50 million, ndiye bwezi ndili ku Malawi kuno?” Atero a Chisingaa.

A Chisinga omwe a kuti anakhalapo wa polisi, atsutsaso zomwe apolisi akunena kuti iwo anamulanda wa polisi mfuti pa nthawi yonwe ankafuna kuwamanga ponena kuti wapolisiyo anasiya mfutiyo pansi zomwe zinawapatsa mpata kuti iwo angotola mfutiyo ndipo atinso iwo amaombera dala pambali chifukwa samafuna kupha munthu.

“Wapolisiyu anali osasamala, anayisiya mfutiyo pampando wa thilaki yomwe ndimayendetsayo. Nde chifukwa choti zimandiwawa kuti sindikuyenera kumangidwa pamene sindinalakwe, ndinangotenga mfutiyo ndikuyitchera kenaka ndinumuza kuti suntha nde ankapanga makani kenaka ndinaomba kawiri. Sindimafuna kuti ndimuphe, ndinakafuna nkathaso kumupha bwinobwino. Ndinamuuza wa njinga kuti anditenge, ndinathawa ndi mfutiyo chifukwa ndinakayisiya anakatha kundiombera.

“Nditathawa ndinamuimbira Kaferenjimbula (wa polisi) ndinamuuza kuti futi yanu ndikupatsani, ine sindimayenda ndi mfuti, siine wakuba. Kenaka ndinakayisiya pa chitsime pa polisi paja kuti atenge mfutiyo,” anateloso Chisinga.

Pakadali pano mkuluyu wadandaula kuti apolisi a pa Kanengo akumuyipitsira mbiri kuti iye anasiya ntchito ya polisi cholinga azibera anthu zomwe wati ndi bodza la mkunkhuniza.

Advertisement