Makosana a MRA abilibinya Jetu – Dorothy Kingston

Advertisement
Jetu

Dorothy Kingston wadandaula zakhalidwe lomwe achita akuluakulu a Malawi Revenue Authority (MRA) komaso apolisi munzinda wa Lilongwe omwe akuti awazunza komaso kumumenya woyimba wachikulire Jetu.

Dorothy yemwe ndi nkazi wake wa woyimba Zeze Kingston, wati gogo wa zaka 72-yu pamodzi ndi iye akumana ndi tsokali Lachinayi madzulo pomwe amabwelera ku Blantyre kuchokera ku Lilongwe komwe Jetu anapita kukalandira malo omwe wapatsidwa ndi kampani ina. 

Mayi Kingston omweso amadziwika ndi dzina loti Cash Madam, alemba patsamba lawo la fesibuku kuti cha m’ma 3 koloko masana, akuluakulu a MRA anawalanda galimoto yawo pomwe amadutsa malo ochitira chipikisheni a Nathenje paulendo wawo waku Blantyre.

Dorothy Kingston

Iye wati apolisi molamulidwa ndi a MRA, anawalanda galimotoyi yomwe amayendera ponena kuti ilibe zoziyenereza zina monga mapepala ndipo akuti galimotoyo pamodzi ndi iwo, anatengeledwa ku ofesi ya MRA komwe akuti zinthu zinafika povuta kwambiri. 

Iwo ati momwe nthawi inali cha m’ma 8 koloko usiku, analamulidwa kuti pamodzi ndi Jetu atuluke ku mpanda wa MRA asiye galimoto yawo yomwe amati ili ndi milandu. 

Mayiyu wadandaula kuti m’modzi mwa akuluakulu a MRA anamuponda Jetu ku nsana mpaka kumugwetsa pansi zomwe wati ndi nkhaza kwa gogoyu.

“Nthawi yokwiyitsa kwambiri inali pomwe Jetu anapondedwa kunsana ndipo anagwa pansi ndikuyamba kulira. Apa ndipomwe ndinalephera kupilira ndipo ndinadzudzula apolisi kaamba kochitira nkhaza Jetu komaso ine ndipo anatitulutsa panja, kuika miyoyo yathu pa chiopsezo,” wadandaula Dorothy. 

Cash Madam ati chodabwitsa nchakuti atachitilidwa nkhaza zosezi, pomwe nthawi imathamangira 9 koloko usiku, anaitanidwa ndi wa polisi wa chitetezo ku ma ofesi a MRA-wo yemwe akuti anawauza kuti alowe mumpandamo akatenge galimoto yawo ponena kuti inalibe vuto lili lonse. 

Dorothy wati akukhulupilira kuti MRA ikudziwa kuti inawalanda galimoto mosatsata malamulo, ayipitsilidwa mbili, awazunza komaso awalepheretsa kupanga zinthu zina zaphindu zomwe amayenera kupanga.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.