Bambo wamangidwa kamba kokakamiza mnyamata kumuyamwa maliseche

Advertisement
Malawi24

A Polisi m’boma la Balaka amanga bambo wina wazaka 38 kamba kokamiza nyamata wa zaka zisanu kuti amuseweretse ndi kumuyamwa maliseche ake.

Malinga ndi kalata ya apolisi yomwe ikuzungulira m’masamba anchezo osiyanasiyana, bambo oganizilidwayu ndi a Kefasi Kambanizithe omwe achita kusaweluzikaku kumayambiliro kwa sabata ino m’mudzi mwa Harry.

Kalata ya a Polisiyi ikusonyeza kuti bamboyi anakumanizana ndi mwanayu yemwe amayendera zake ndipo atamuyimitsa anamuvula ndikuyamba kumuyamwa maliseche mwanayo.  

Atamaliza kumuyamwa mwanuyu, bambo wothothoka nsidzeyu anamukakamizaso mwanayu kuti nayenso amuyamwe maliseche ake kwinaku akumuopseza kuti akayelekeza kukuwa amuthyolathyola.

Pamapeto pa zomwe amafunazo, bambo Kambanizithe anamupatsa mwanayu MK100 ngati yomutsekera pakamwa kuti asauze munthu aliyese. Mwanayu analephera kupilira ndi malodzawo kotelo anauza makolo ake.

Nawo makolo ake sanachite chidodo koma kuthamangira ku Polisi kukadandaula za nkhaniyi ndipo nawo apolisi sanachedwe koma kukhazikitsa kafukufuku womusaka mkuluyu kufikira pomwe wamangidwa Lachitatu.

Kefasi Kambanizithe yemwe amachokera m’mudzi wa Chilobwe, dera la Kachenga m’boma la Balaka, akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu opanga nkhanza ndi zosayenera ndi mwana. 

Advertisement