Zitengera a Malawi kukavotera mtsogoleri  wanzeru – Watero Lungu

Advertisement
Edgar Lungu

M’tsogoleri wakale wa dziko la Zambia, a Edgar Chagwa Lungu, wati zitengera a Malawi kukavotera m’tsogoleri amene ndi wongoyeselera zinthu kapena wodziwa zinthu, maka pachisankho chomwe chichitike chaka chamawa m’dziko muno.

A Lungu ayankhula izi pa tsamba lawo la m’chezo la Fesibuku dzulo pa 16 May 2024.

M’mawu ake lungu anati akumva kuti a Malawi adzavota chaka chamawa ndipo anthu ambiri adzasankha pakati pa paukadaulo pochita zinthu kapena kungochita zinthu moyeselera.

Pomaliza a Lungu anati akufunira zabwino abale ndi alongo kuno ku Malawi ndipo iye analangiza anthu m’dziko muno kuti akhale amtendere komanso otetezeka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.