Bambo wadzipha ataba nkhuku

Advertisement

Bambo wa zaka 38 mu mzinda wa Lilongwe wadzipha podzimangilira  ku denga la nyumba yake atazindikira kuti abale ake adziwa kuti iye anaba nkhuku ya m’bale wake.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya munzinda wa Lilongwe mayi Khumbo Sanyiwa omwe azindikira malemuwa ngati a Davison Sitima.

Sanyiwa wati bambo Sitima akuwaganizira kuti anaba nkhukuyo m’mawa wa pa 4 November chaka chino m’mudzi wa Chembekung’ombe komwe amakhala.

Ofalitsa nkhaniyu wati malemu Sitima pa tsikulo anaba nkhuku ndi kuibisa m’malaya n’kumalowera nayo ku mtsinje, koma pa njira adakumana ndi mnyamata wina yemwe adaona n’kukanena kwa azibale awo.

Apolisi ati mkuluyu atafunsidwa za nkhaniyi, adavomera kuti anabadi nkhukuyo ndipo adayibweza kwa mwini wake yemwe akuti ndi nsuweni wake.

Patadutsa nthawi yochepa, bambo Sitima adapezeka atadzimangirira m’nyumba mwawo ndipo potsatira za chipatala cha Nathenje zasonyeza kuti mkuluyu adamwalira kaamba kolephera kupuma kutsatira kudzimangilirako.

Davison Sitima amkachokera m’mudzi wa Chembekung’ombe, kudzera la mfumu yaikulu Kalumba m’boma la Lilongwe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.