Mlonda wanjatidwa ataba zida zoyimbira m’tchalitchi chomwe amalondera

Advertisement
CUFF

A polisi munzinda wa Lilongwe akusunga mchitokosi mlonda wa zaka 44 wa mpingo wa Time of God pomuganizira kuti anathyola kachisicho ndi kuba zida zoyimbira za ndalama zoposa K3.5 miliyoni. 

Wofalitsa nkhani za polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu, atsimikiza za nkhaniyi ndipo azindikira oganiziridwayu ngati a Patrick Zgambo omwe akuti anapanga chipongwechi kumayambiliro a sabata ino.

 A Chigalu ati nkuluyu amalondera tchalitchichi ngati ogwira ntchito wa kampani ina yopeleka chitetezo ndipo akuti wamangidwa Lachitatu pa 15 May, 2024 pomwe ananyamula katunduyu pa njinga.

A polisi ati m’bandakucha wa tsikuli, mkuluyu anangoti gululu ndi a polisi omwe amachita chipikisheni msewu wa Kamuzu Procession ndipo atamufusa zokhudza katundu yemwe anayamulayo, Zgambo anayamba chibwibwi zomwe zinakayikitsa apolisiwo.

Apa apolisiwo anamupanikiza mkuluyu ndi mafuso mpaka pomwe anaulura kuti anaba katunduyu ku tchalitchi cha Time of God yomwe ili mbali ya ku Palm Lock, moyang’anizana ndi sukulu ya Ukachenjede ya Kamuzu School for Health Sciences.

Mkuluyu anawulura kuti pa tsiku lomwe ankagwira ntchito anathyola zenera lalikulu la kachisicho ndikulowa nkubamo zida zoyimbira zomwe ndikuphatikizapo 16 channel mixer, ma mayikolofoni 6 ndi zoimikira zake, ma ampulifaya ndi zinthu zina.

Woganiziridwayu yemwe amachokera m’mudzi mwa Mzikubola, mfumu yayikulu Mabulabo, m’boma la Mzimba akuyembekezeka kukawonekera ku khothi posachedwapa komwe akayankhe mlandu wothyola nyumba komaso kuba katundu.

Advertisement