Olira samugwira pakamwa ndipo mneneri wakale wa chipani chotsutsa cha DPP, a Nicholas Dausi, walira mokweza pa mwambo wa maliro wa a John Tembo.
Poyankhula pa bwalo la za masewero la Dedza pamene amaimilira anzawo a Kondwani Nankhumwa amene ndi mtosgoleri otsutsa mu nyumba ya malamulo, A Dausi anati a Tembo anali katakwe pa ndale.
Malinga ndi a Dausi, ukadaulo wa bamboo Tembo pa ndale unaonetsedwa pamene anagwira chipani cha Kongeresi.
“A Tembo anali dolo pa ndale,” anatero a Dausi. “Ndipo iwo samangochotsa anthu mu chipani iyayi.”
A Dausi anayankhula izi pamene iwo ali mu mkokekoke ndi chipani chawo cha DPP chimene chinawathothola. Ambiri amayesa izi zinachitika chifukwa a Dausi anapezeka akukondwa, mpaka kuvina, pa msonkhano wa Kongeresi kumene anakhalitsako ngati membala mpaka anakhalapo wachiwiri kwa a Tembo.
“Ine ndinagwira ntchito ndi a Tembo komanso a Kamuzu Banda. Olo ukayenda nawo ulendo wa kunja, zimaonetsa kuti Tembo ndi katswiri. Wekha umadziwa kuti apa pali munthu apa,” anaonjezerapo chotero a Dausi.
Thupi la a Tembo layikidwa mmanda lero kwawo ku Dedza. Iwo adamwalira ku Lilongwe atadwala kwa nthawi matenda a shuga. Pa ena omwe anali pa mwambo wa maliro ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera komanso mtsogoleri wakale a Bakili Muluzi.