Samalani uko! A ma truck aopseza kuti anyanyalanso ntchito

Advertisement
Striking Truck Drivers in Malawi

Palibe kopumira. Ngati a boma akuti mafuta akusowa chifukwa palibe ndalama za kunja, pompano aonjezekera kusowa chifukwa sipakhala owanyamula. Onse oyendetsa galimoto zikuluzikulu ati kuyambira pa 18 apa ayamba kunyanyala ntchito.

Malinga ndi Malipoti, madalayivalawa ati ndi osakondwa kuti mavuto amene akhala akukumana nawo sanakonzedwe ndipo ena angoonjezekera.

Mtsogoleri wa bungwe loyang’anira madalayivalawa a Mphatso Molleni auza nyumba zoulutsira Mawu kuti ena mwa mavuto amene akukumana nawo ndi oti sakupatsidwa mswahala akagwira ntchito mopyolera muyezo. Atinso akuvutika kupeza zitupa zoyendetsera maka pano pamene boma linaimika kaye ntchito yopanga zitupazi.

A Molleni ati ulendo uno kunyanyala kwawo kukhala kwa mnanu chifukwa sadzilora ndi komwe kuti ngakhale oyendetsa ma truck a m’maiko ena azibwela ku Malawi ndi katundu wawo.

Advertisement