Anthu a mdera la Ntiya Ward awapempha azavotere khansala wa UDF

Advertisement
Lilian Patel (L) and Ntiya Ward candidate Fatima Thewe during a campaign rally in Zomba

Mtsogoleri wachipani cha UDF Mai Lillian Patel wapempha anthu a mdera la Ntiya Ward mu mzinda wa Zomba kuti adzavotere khansala wachipani cha UDF pa chisankho chachibwereza chomwe chizachitike pa 26 mwezi uno.

Mai Patel amayankhula izi Lamulungu ku Ntiya Ward pomwe chipani cha UDF chidachititsa msonkhano wokopa anthu kuti adzavotere khansala wachipanichi Fatima Thewe.

Iwo adati khansala ndi wofunika kwambiri pankhani yachitukuko choncho ndikofunika kuti anthu a Ntiya Ward akavotere Fatima Thewe yemwe ndi wachipani cha UDF chifukwa ndiyekhayo yemwe angabweretse chitukuko mdelaro.

A Patel adapemphanso anthu kuti asamale ziphaso zawo zovotera komanso ziphaso za unzika popeza pali anthu ena omwe akumatenga ziphaso powanamiza kuti awapatsa ndalama.

Pamenepa Mai Patel, adati chipani cha UDF chidalamulira m’dziko lino kwa zakha khumi (10) ndipo adati mu nthawi yawo adapanga zitukuko zosiyana siyana mu mzinda wa Zomba monga miseu yabwino, sukulu komanso adamanga Dam la Mulunguzi lomwe likupereka madzi awukhondo okumwa mu mzindawu choncho ndichifukwa chake akupempha anthu kuti adzasankhe khansala wachipani chawo.

“Khansala ndiyemwe amabweretsa zitukuko kudzera ku khonsolo chifukwa MP ntchito yake ndikupanga malamulo kunyumba ya malamulo choncho ndikupempheni kuti mudzatsankhe Fatima Thewe kuti adzakubweretsereni zitukuko zosiyana siyana kuno,” adatero Mai Lillian Patel.

Ndipo poyankhulapo, yemwe akudzayimira ngati khansala wachipani cha UDF mdera la Ntiya Ward pachisankho chikubwerachi Fatima Thewe adati akadzamusankha adzayesetsa kudzabweretsa zitukuko zosiyana siyana monga kumanga miseu yabwino ndipo adapempha anthu kuti adzamuvotere popeza ndiwochokera mdera lomwelo.

Chisankho chachibwerazachi chikuchitika potsatira imfa ya Khansala Ramsey Kajosolo yemwe adali wachipani cha UTM.

Advertisement