Wanderers yamwa wa mkaka

Advertisement
Wanderers

Ayi ndithu lero mu Tnm Super League zavutirapo ndithu pamene imodzi yokha ndiyo yaluza pamene ena anayi afanana mphamvu pakutha kwa masewero lero pa 11 May 2024.

Mighty Mukuru Wanderers yamwa mkaka wa ngambwingambwi pomwe yaswa anyamata a Karonga United. Tikunena kuti Wanderers yaumbudza anyamata a Karonga United ndi chigoli chimodzi kwa duuu.

Nayo Mafco imayembekezera kumwa wa mkaka koma ayi ndithu zavutirapo pamene Maule, Nyasa Big Bullets inabweza kumapetopeto. Inde inu paja amati Maule mkumadzulo, Bullets 1, Mafco 1. 

Anyamata a Civo United afanana mphamvu ndi anyamata a Bangwe All Stars ndipo masewero athera 1 kwa 1.

Moyale Barracks yalepherana ndi anyamata a Chitipa United pa bwalo la masewero la Mzuzu ndipo masewero athera 1 kwa 1.

Anyamata a Baka City alepherananso ndi anyamata a Fomo ndi chigoli chimodzi kwa chimodzi.

M’menemo ndimo masewero athera lero mu Tnm Super League.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.