Osaletsa munthu odwala matenda a HIV ndi EDZI kumwa mankhwala – atero a chipembedzo

Advertisement
ARVs

Chipembedzo ngati gawo lina lomwe limathandiza anthu omwe anapezeka ndi Matenda a HIV ndi EDZI kupitiliza kumwa mankhwala awo mwandondomeko, ati sibwino kuletsa  munthu odwala nthendayi kumwa mankhwala mwandondomeko.

Mpingo wa Holy Trinity kudzera mwa Mneneri David Nkhondo wati ngati mtsogoleri yemwe amalandira komanso kukumana ndi anthu osiyanasiyana ndipo ena mwa iwo n’kukhala amene anapezeka ndi nthendayi, ati amayesetsa kulimbikitsa odwalawa kumwa mankhwala mwandondomeko yoyenera.

A Nkhondo anawonjezera ponena kuti chipembedzo ndi mbali ina yomwe imathandidzira anthuwa kuti akhale okhulupirika pamalemba komanso asataye mtima moyo wawo wathupi komanso wauzimu.

Iwo adatinso kuletsa munthu kupitiliza kumwa mankhwala ake sikoyenera kutero potengera kuti a chipatala amakhala apereka uphungu oyenera kwa munthuyo ndipo ngati a chipembedzo  akuyenera kuthandiza achipatala kumbali ina yolimbikitsa odwala nthendayi kuti apitilize kumwa mankhwala.

Mlembi wa wankulu wa bungwe la chipembedzo cha Chisilamu a Abbas Vinjenje anati ku chipembedzo chawo, amalimbikitsa osatira chipembedzochi kuti asasale odwala nthenda ya HIV ndi EDZI popangira zinthu zonse limodzi kuti asamakhale ndi maganizo ena aliwonse.

A Vinjenje anapitiliza ponena kuti aliyense wa chipembedzo chilichonse akuyenera kutengapo gawo lothandizira odwala nthendayi kumwa mankhwala mwandondomeko komanso powalimbikitsa munjira zosiyanasiyana.

M’chikalata chomwe Mkulu wa bungwe la National Aids Commission (NAC) Beatrice Lydia Matanje anatulutsa, anadandaura komanso kukhudzidwa ndi mauthenga a malonda  ochuluka okhudzana ndi machiritso a HIV ndi EDZI omwe akumafalitsidwa kwambiri.

Matanje anati m’dziko muno kulibe mankhwala ochiza nthendayi ndipo chithandizo chilipo padakali pano ndi kumwa mankhwala otalikitsa moyo (ma ARV) omwe amagwira ntchito yoletsa kuchulukana kwa HIV m’magazi a anthu omwe anapezeka nayo.

Aliyense wochita motsutsana ndi Ndime 25 ya lamulo lothandizira kukhazikitsa ndondomeko za kapewedwe ndi ntchito zolimbana ndi muliri wa HIV ndi EDZI , amayenera kulipira chindapusa cha 5 miliyoni kwacha  ndi kukhala kundende kwa zaka zisanu koma ngati ndi bungwe, likuyenera kulipira chindapusa cha 10 miliyoni kwacha.

Advertisement