Wayamba kampeni Mutharika, ali pa Njamba mawa lino


Mutharika

Mtsogoleri wa chipani cha DPP, a Peter Mutharika amene owakonda amangoti APM, akuyembekezereka kugwedeza mzinda wa Blantyre mawa lino pa 12 May. A Mutharika amene akhala nthawi osachititsa msonkhano wandale alengeza kuti akhala pa Njamba Freedom Park.

Malinga ndi tsamba lawo la Facebook, iwo ati akubwera pa Njamba kuti afotokozere a Malawi mfundo zawo za chitukuko maka pano pamene alengeza kuti ayimanso.

Msonkhano wa a Mutharika ukubwera pamene kwabwera chipani china chatsopano cha PDP chomwe akutsogolera ndi a Kondwani Nankhumwa omwe anathamangitsidwa mu chipani cha DPP. A Nankhumwa adati akhala akuchita misonkhano m’madera osiyanasiyana mu dziko muno kukhazikitsa chipani chawo. Ena akuyesa kuti a Mutharika akuchititsa msonkhano wawo pofuna kukhala patsogolo.

A Mutharika, amene amakhala ku Mangochi, alengeza kuti ali ku Blantyre kukonzekera msonkhano wawo umene autchula kuti mega rally.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading