“Tikupititse kwa sing’anga kapena ku mapemphero?” – Gibo Pearson wakwiyira Gwaladi

Advertisement

Zitsulo kunolana: Oyimba Giboh Pearson walangiza oyimba nzake Joe Gwaladi kuti achepetse uchidakwa, ndipo wamuuza kuti asankhe kumutengera ku mapemphero kapena kwa a sing’anga.

Nkhaniyi yadza potsatira kanema yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo yomwe ikuonetsa Gwaladi atapana mkazi pa malo ena omwela chakumwa cha ukali.

Mu kanemayo, Gwaladi yemwe amaoneka kuti wandongwa, akuoneka akugwiragwira mabere a mkazi yemwe anapanayo kwinaku kanyimbo kakuveka cha pansipansi ndipo anayankhula kuti mkaziyo sangapose akazi aku South Africa komwe anapita posachedwapa.

Kanemayu wakwiyitsa Pearson yemwe ndi ponda apa nane mpondepo wa Gwaladi, ndipo wadzudzula nzakeyu kaamba kochulukitsa chibwana.

Masiku apitawa, Pearson wa Phalombe music anamutchayira lamya Gwaladi yomudandaulira kuti achepetse kumwa mowa mwauchidakwa kaamba koti akaledzera akumapanga za umoya zomwe wati sizoyenera potengera kuti iye ndi otchuka.

Munkucheza kwawo pafoni yomwe Pearson anaimba, Gwaladi akuonetsa kuti sakudziwa kuti china chitika ndi chiyani ndipo kangapo konse oyimbayu anakanitsitsa mwantu wa galu kuti sanapane nkazi aliyese.

“Pearson: Ase iweyo vuto lako ndi chiyani koma? Gwaladi: zakhala bwanji? Pearson: zakhala bwanji, tiziti sukudziwa chomwe chachitika? Koma mutu wako umagwira? Kodi iweyo ukufunika tikupititse kwa a sing’anga kapena ku mapemphero? Gwaladi: zakhala bwanji tandiuze?

“Pearson; Mesa kwatuluka ka vidiyo kakuyenda mmafonimu, iweyo umagwira gwira mabere andani…. Gwaladi Mesa ndi mkazi oyimba kuja timagona kuja? Thandie wa ku South Africa kuja tinafikira ifeyo kuja.

Pearson:ayi siameneyo. Gwaladi; eee nde ndiutiso nkazi ameneyo?

Pearson: Ndimakuuzani muzizisungira ulemu, tsono ndikakuyankhulani mumakhala ngati mwamva. Mukaledzera mumapanga zopoira nkuiwala kuti anthu amakhala akukujambulani,” inali choncho mbali ina ya macheza a Pearson ndi Gwaladi.

Pearson wamuuza Gwaladi kuti zomwe akupangazo zili ndikuthekera koti atha kuluza nazo anthu omukonda ndipo wati oyimba nzakeyu achepetse kuledzera ngati akufuna kuti anthu azimukondabe.

Pakadali pano anthu ayamikira Pearson pomukhalira pansi nzakeyu koma ena amudzudzula Pearson kaamba kofalitsa zomwe anayankhulana pafoni ndi Gwaladi.

Advertisement