Mulandu wa sing’anga ogwililira atsikana anai uzapitilira pa 2 May

Advertisement

Bwalo la milandu ku Zomba lizapitiriza mwezi wamawa kumva mulandu wa sing’anga wina Malizani Pawoneke Salizeni yemwe akumuganizira kuti anagwililira

atsikana anai achichepere osakwana zaka 17.

Malizani Pawoneke Salizeni yemwe ndiwa zaka 23 zakubadwa adapalamula mulanduwu m’mudzi mwa Diamond mdera la Sub T/A Ntholowa Boma la Zomba.

Majistileti Martin Chipofya wayamba wayimitsa mulanduwu mpaka pa 2 May pomwe mbali ya Boma idzapitilize kubweretsa mboni zake ndipo Lachiwiri mboni ziwiri ndizomwe zidabwera kudaperekera umboni.

Pakalipano Sing’anga Malizani Pawoneke Salizeni adakali mmanja mwa a Police ndipo akumusungabe ku ndende yayikulu ya Zomba.

Iye akumuganizira kuti anakwatira atsikana anai achichepere ndipo anagona nawo ndikuwapatsa matenda.

Follow us on Twitter:

Advertisement