Chikhulupiliro cha Habakkuk n’chosuntha phiri

Advertisement
Prophet Habakuk

Patangodutsa sabata imodzi pomwe Prophet Shepherd Bushiri adapeleka ndalama zokwana 6 miliyoni kwacha kwa ‘M’neneri’ Habakkuk kutsatira pempho lomwe adapereka, lero Habakkuk wapemphanso thandizo lina kwa m’neneli Bushiri.

Mneneri Habakuk ati akufuna thandizo loti amangire nyumba ya zonse mom’mo ya zipinda zokwana 8 komanso thandizo lomangira ma boyizikota okwana 10 kapena 7 okhala ndi zipinda zitatu iliyonse omwenso ndi azimbudzi mkati komanso malo osambira.

Habakkuk wanena izi kudzera mkanema emwe Malawi24 yaona ndipo malingana ndi kanemayu, Habakkuk akufotokoza za momwe iye adagwilitsira ntchito ndalama yomwe adapatsidwa, ndipo iye wati ndalama zokwana 1 miliyoni wazisunga ku banki, 1 miliyoni ina wagawa kwa achibare, pamene ndalama zokwana 3,450,000 wadzala poyigulira malo.

Mneneri Habakuk

Iye wati malo omwe wagulawo akufuna amangepo nyumba ya zonse momo ya zipinda zokwana zisanu ndi zitatu (8) yokhala ndi makonde akuluakulu awiri. Kuphatikiza apo, iye wati akupemphanso thandizo lomangira nyumba zocheperako pachingerezi amati maboyizikota omwe wati akufuna atamanga okwana 10 kapena 7 ndipo maboyizikotawa akufuna azakhale azipinda zitatu komanso azimbudzi momwemo.

Iye anafotokoza kuti zonsezi zichitike chaka chino ndipo pakadali pano akufuna njerwa ziyambe kuumbidwa kuti amangire nyumbayo.

Iye wapemphanso mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus Chakwera, a m’neneri Bushiri, a Mikozi, a Zodiak, a MBC ndi ena kuti a muthandize kumanga zinthuzi.

Pakadali pano, pempho lomwe Habakkuk wapereka ladzetsa mpungwepungwe m’masamba am’chezo pomwe ena akuti mkuluyi akufunika kuyezedwa misala mokakamiza pamene ena akuti mkuluyu ndi osayamika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.