Bangwe yadya wani, Zonke watekesa ndi nyimbo ya tsopano 

Advertisement
Zonke Too Fresh

Pamene anthu asanamalize kusimba za woyimba Jetu yemwe amachokera ku Bangwe munzinda wa Blantyre, woyimba winanso ochokera ku delari, Zonke Too Fresh, walowa m’bwalo ndi nyimbo yake ya tsopano yomwe akuyitchula kuti ‘Vote’. 

Zonke Too Fresh, yemwe dzina lake leni leni ndi Zaithwa Mhone, watulutsa nyimbo yatsopanoyi Lachiwiri m’mawa ndipo nyimboyi yatulutsidwa pamodzi ndi kanema yake yemwe yathyakulidwa mwalunso. 

Munyimbo yachikondiyi, Zonke  akuwuza nyenyezi yomwe yamudolora mtima kuti ipange chisankho chosankha iye yekha ngakhale kuti pali njonda zina zomwenso sizikupuma naye bwino. 

“Azimayi avale zitenje, nthawi ya kampaleni/Anyamata muzipente, tikumane mu nsewu/Popita tikwera lole, amayi patsogolo/Koma amene asalore, sitimulemba za ngongole/Ndipatse bwalo apa, chisankho changa ndapanga, mtimawu nawo ndasankha/Izi zinazo zitaye/Vote yaine ili muntima,” ikumatelo ndime yoyamba ya nyimboyi. 

Poyankhula ndi tsamba lino, Zonke yemwe chaka chatha anatekesa ndi nyimbo ya ‘Kambuzi’, walonjeza kupitiliza kusangalatsa a Malawi ndi nyimbo zosangalatsa komanso zophunzitsa.

“Choyamba ndikufuna ndithokoze anthu onse omwe amakonda nyimbo zanga. Sapoti yawo ndi yomwe yandithandiziranso kuti ndikwanitse kutiulutsa nyimbo iyi ya Vote. Zabwino zikhala zikubwerabe kutsogoloku,” watelo Zonke Too Fresh. 

Woyimbayu, yemwenso chaka chatha anapambana mphoto ya MBC Entertainers of the year, wati ali ndichikhulupiliro kuti nyimbo ya ‘Vote’ ikhala yokondedwa kwambiri. 

Pomwe pamatha maola asanu kanema ya nyimboyi ataponyedwa pa YouTube, anali ataoneledwa kale ndi koposa ka 20 sauzande chomwe ndichisonyezo kuti anthu ambiri agwa nayodi mchikondi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.