Wanderers yakong’ontha Silver Strikers

Advertisement
Wanderers vs Silver strikers

Mu masewelo a mpira wa miyendo  okumbukira tsiku la mtsogoleri oyamba wa dziko lino a Ngwazi Dr Hastings Kamuzu Banda pakati pa Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers  pa Kamuzu stadium athela kukomera Wanderers.

Mphunzitsi wa timu ya Silver Strikers, Peter Mponda wati  masewero a alero sanali masewelo abwino kweni-kweni ponena kuti  mipata yomwe anzawo anapeza akwanitsa kuwagonjetsa koma masewelowa asapusitse anthu.  

Wanderers kuthambitsa Silver Strikers pa Kamuzu Stadium.

Naye Meke Mwase wachiwiri kwa mphunzitsi wa  Mighty Mukuru Wanderers wati ndi okondwa ndi chipambanochi, zinangovuta kuti anyamata ake ambiri omwe asewera lero nkoyamba kusewera maselo a mphamvu. 

Masewelowa omwe anali ndi mphindi 25  mchigawo  chilichonse athela mokomela anyamata a ku Blantyre a Manona  chigoli cha Fransisco Madinga  pa mphindi ya 16 mchigawo choyamba.

Awiriwa akumananso kumathero kwa sabata ino mu chikho cha TNM pamene akutengetsana Silver ikutsogolera ndi Wanderers pa nambala yachiwiri pa mndandanda wa ma timu a mu ligiyi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.