Chakwera alamulira 2030 woo, atero a Chimwendo-Banda

Advertisement

Nduna yowona za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda ati amene akulota kuti alowanso m’boma apitilize kulota kamba koti m’tsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera alamulira mpaka 2030.

Ndunayi yayankhula izi pa chikondwelero chokumbukira mtsogoleri oyamba wadziko lino Malemu Ngwazi Dr. Hastings Kamuzu Banda ku Blantyre pa Kamuzu Stadium.

A Chimwendo anati Kamuzu anali mtsogoleri okonda anthu onse ndi chifukwa chake anapanga zitukuko zambiri dziko lonse.

Iwo anapitiliza kunena kuti a Chakwera akuyenda m’masomphenya a Kamuzu ndipo akukweza maphunziro mdziko muno ndi zina zambiri

“Ena akuganiza kuti alowanso m’boma, awo ndi maloto a chumba, ndizosatheka, Chakwera alamulira mpaka 2030 woo palibe omuchotsa,” anatero a Chimwendo Banda.

Chilima kupereka moni kwa Mama Kadzamira.

Ndunayi inatinso mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika akuyenera afotokoze ku mtundu wa aMalawi chimene anayiwala ku Nyumba za  boma.

M’mawu ake mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wati Kamuzu anapanga zitukuko zambiri ku Blantyre kuphatikizapo ma sukulu a ukachenjede, nyumba, komanso Kamuzu Stadium mwa zina.

M’tsogoleriyu wati salora anthu andale omwe amakonda ndale zogawanitsa aMalawi awasokoneze kuchita zitukuko mdziko muno.

“Olo anthu opanga ndale zogawanitsa aMalawi afune asafune ine sindisiya kupanga zitukuko mdziko muno. Sindisiya kumanga nyumba za anthu achitetezo, zipatala, miseu ndi ma bridge, kupereka K200 million ku constitutency ili yonse mmalawi muno ya chitukuko,” anatero a Chakwera.

Pa chikondwererochi panali magule, zolankhula zosiyana siyana ndi masewero apakati pa Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers, pomwe Silver Strikers yagonja kwa Wanderers pachigoli chimodzi kwa duu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.