Anthu m’dziko muno akudzudzula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera pabodza lankunkhuniza lomwe wayankhula kuti boma la Tonse lapanga ntchito zoposa 900,000.
Potsekulira nyumba ya malamulo Lachinayi mumzinda wa Lilongwe a Chakwera anatutumutsa anthu pomwe anati boma lawo lakwanitsa kupanga ntchito zokwana 997,423 mumzaka ziwiri.
A Chakwera omwe nthawi yokopa anthu kuti awavotele analonjeza kuti adzapanga ntchito chikwi (1million) mu mchaka choyamba cha ulamuliro wawo, anati chosangalatsa kwambiri ndichoti izi zatheka ngakhale dziko lapansi lakhudzidwa ndi matenda a COVID-19.
Koma poyankhulapo pankhaniyi, mkulu wa bungwe la anthu ololemba anthu pa ntchito la Employers Consultative Association of Malawi (ECAM) a George Khaki, ati zomwe ayankhula a Chakwera ndi nkhambakamwa chabe.
A Khaki omwe amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsira mawu mdziko muno, ati ngati a Chakwera akufuna kuti anthu awakhulupilire pa zomwe ayankhulazi, akuyenera apeleke umboni wake.
Mkuluyu wati mu umboni omwe mtsogoleri wa dziko linoyu apeleke pa zomwe wanenazi, akuyenera kufotokoza tsatanetsatane wa anthu komaso malo omwe anthuwo alembedwa ntchito zikunenedwazo.
“Chuma chadziko lino chikupitilirabe kukumana ndimavuto ankhaninkhani. Kaamba ka mlili wa COVID-19, tawona ntchito zamalonda zikulowa pansi mdziko muno komaso ndalama yathu ikutsika mphamvu.
“Choncho ndikuganiza kuti zomwe anenazi zitabwera ndi umboni wake owonetsa mwatsatanetsatane anthu omwe alembedwa ntchitowa, komaso malo enieni omwe alembedwa ntchito, zitha kukhala zosangalatsa,” atero a Khaki.
A Khaki anati chodabwitsa kwambiri mchakuti posachedwapa a Chakwera anauza dziko lapansi pomwe ankayankhula ndi wailesi ya BBC kuti a Malawi oposera 600, 000 anachotsedwa ntchito.
Kupatula ndemanga ya a Khaki, a Malawi ochuluka makamaka pamasamba amchezo adzudzula a Chakwera ponamiza anthu pa chiwerengero chenicheni cha anthu omwe alembedwa ntchito pa zaka ziwiri zaulamuliro wawo.
A Henzie Mulole omwe anaikira ndemanga pankhaniyi patsamba lathu la Facebook anati: “A Chakwera akuganiza kuti ndife opusa. Atha kunama kudziko koma sanganame kwa ovota. Pena ndibwino kungokhala chete koma poti amakonda kuyankhula, ayankhuladi momwe angathere koma akuiwala kuti nthawi ikutha komaso kuti ife tikuwaona,”
Naye Dorah Chisale anati a Chakwera asapusitse anthu kuti boma lawo lalemba ntchito anthu oposa 900,000 ponena kuti mtsogoleriyu wangolemba ntchito apa banja pake osati a Malawi.
Mwandemanga zoposa 500 zoyambilira pa nkhaniyi, ndemanga zoposa 400 zimadzudzula a Chakwera ponama pa kulembedwa ntchito kwa anthu 900,0000 pemene ndemanga zinazo zinali zowayamikira a Chakwera.