Atupele Muluzi akuti pakali pano opambana zisankho sanapezeke

Advertisement
Atupele Muluzi

A Atupele Muluzi omwe ndi achiwiri kwa a Peter Mutharika pa zisankho za pulezidenti za chaka chino apempha a Malawi kuti asamvere mphekesera chifukwa pakali pano palibe yemwe wapambana zisankhozi.

A Muluzi ananena izi lero pa a msonkhano wa atolankhani womwe anapangitsa kuti Blantyre. Malingana ndi a Muluzi, mtsogoleri wa dziko lino a Mutharika ndi omwe anawauza ktui apangitse msonkhanowu.

Iwo anati bungwe la chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ndi lomwe lili ndi udindo wolengeza opambana kapena olephera ndiye  bungweli silinamalize ntchito yotsimikiza zotsatira zachisankho.

“Pali mphekesera zonena kuti pali opambana pa chisankho chimenechi komanso pali mphekesera kuti pali amene walephera.

“Tikupempha kuti tonse tikhale mtima m’malo, tisathamange kumvera mphekesera. Tiyeni tidikire kuti bungwe la MEC limalize ntchito yake kuti pamapeto pake tikhale ndi mtsogoleri ovomelezeka ndi a Malawi onse,” anatero a Muluzi.

Iwo anaonjezera kuti mphekesera zomwe zilipo zokhudzana ndi chisankho zikusokoneza bungwe la Malawi Electoral Commission.

A Muluzi anapempha otsatira zipani za UDF ndi DPP kuti asakhale ndi nkhawa komanso apitirize kukhala pa mbuyo pa a Mutharika. Iwo anauzanso otsatirawa kuti asunge bata ndi mtendere.

A Malawi anaponya voti pa 23 June ndipo bungwe lachisankho silinalengeze zotsatira. Pakadali pano, zotsatira zosatsimikiza zikusonyeza kuti a Lazarus Chakwera a Tonse Alliance ndi omwe apambana zisankhozi.

Advertisement