Chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndikachilombo ka Corona, komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19 , chafika pa anthu makumi atatu ndi mphambu zitatu (33) tsopano.
Izi zachitika patangodutsaso maola ochepa pomwe mlembi wamkulu mu unduna wa zaumoyo, Dr. Dan Namarika mmawa wa lachitatu analengezaso pansonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre kuti anthu asanu ena apezekaso ndi kachilomboka.
Malingana ndi nduna ya zaumoyo m’dziko a Jappie Mhango omwe amayankhula mmawa wa lachinayi, mmaola 24 apitawa, anthu ena khumi (10) apezekanso ndi kachilombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19.
A Mhango ati anthu onse khumi omwe apezeka ndi kachilomboka akuti apezeka m’dera la Kaliyeka mu mzinda wa Lilongwe komwe dzulo kwapezekanso ena asanu ndipo m’modzi mwa asanuwo wamwalira dzulo lomwelo.
Malingana ndi a Mhango anthuwa apezeka ndikachilomboka kaamba koti anakhudzana ndi munthu yemwe wamwalira ndi nthenda ya COVID-19 mdelari ndipo ati palichiopsyezo choti chiwelengelochi chitha kukulabe mtsogolomu.
Apa ndunayi inati pakadali pano ntchito ilimkati yofufuza anthu enaso omwe akuwaganizira kuti akhudzana ndi anthu omwe apezeka ndikachilomboka muderali komaso madera ena ozungulira.
Koma Lachitatu a Namalika anati dziko la Malawi makamaka mzinda wa Lilongwe uli pachiopsezo kuti anthu ambiri atha kupezeka ndi kachilombo ka Corona potsatila kupezeka anthu kwa kachilomboka mmadera omwe mumakhala anthu ambiri ngati Kaliyeka komaso Area 25.
“Izi zabweretsa chiopsezo kwambiri kaamba koti nthendayi yapezeka ndi anthu omwe akuchokera mmadera omwe kumakhala anthu ochuluka ngati ku Kaliyeka komaso ku area 25 zomwe zapangitsa kuti tikhale pantchito yofufuze kuti anthuwa anakhudzana ndindani ndipo chiwerengelochi chitha kunka chikukwelabe,” anatelo a Namarika lachitatu.
Apa tsopano zikutanthauza kuti chiyambireni ntchito yoyeza anthu pa nthenda ya COVID-19, anthu 33 ndiwo apezeka ndi kachilomboka, atatu amwalira ndipo atatu boma linalengeza kuti achira.