Mfumu ya zinyau Limbani Kalilani imene imatchuka ndi dzina lodyera loti Tay Grin yakwera pa chulu ndikunena mokweza kuti anthu abalankhula chifukwa za iyo zinayera kale.
Tay Grin ndiotchuka pa mayimbidwe mu zamba zosiyanasiyana, choncho wagwiritsa ntchito luso lake pouza anthu onse akuthwa pakamwa kuti abayankhula, iyeyo sizikumukhuza. Kudzera mu mayimbidwe ake a tsopano otchedwa Lubwa, Kalilani wanena izi.
Nyimboyo yatuluka patapita masiku ochepa Grin atapambana zikho ziwiri mu Nyasa Music Awards. Iyeyu wanena zinthu zomwe anthu amamunena.
Zina zomwe wanena ndi zoti amake ndi nduna, iyeyo amakwera ndege kawirikawiri, komanso amatchena modetsa nkhawa. Izi sizinasangalase anthu ena pamene anena kuti katswiriyu wadzolera mafuta pa gulu.
“Ndkhumudwa naye koopsa Tay Grin. Zoona azikazitukumula?” Wafusa motero Angali Banda wa Ku Lilongwe
Tay Grin wakhala akutchuka ndi mbiri yoti samayankha anthu akamena zoipa za iyeyo. Koma apa zasonyeza kuti waatopera anthu onse amene akhala akumunena zinthu zosiyanasiyana.
Lubwa yayimbidwa mu chamba cha Ku South Africa chotchedwa house koma sanaiwale kuitendera ndi ng’oma yakwathu kuno. Anthu ena akondwera ndi mayimbidwe amenewa.
“Mkuluyu waonesa luso loti amatha kulowa palipose,” watero Grace Aleck wa ku Lilongwe.
Vomerezani guys.TYG…….amatha..basi.just a matter guys.keep it up man ndi nyimbo zako za bhoozo timakufilani man.
Voto anthu amadama ndi chirungamo, ndi nyimbo zingt zmwe wakhala akumunena kma sanabwezepo moto lero wabweza ubwino wake sadakutchureni dzina ndinthawi yake
Was still puzzles me is that u sing senseless songs koma nkumawina titati tikuike iweo ndi Lulu ….lulu got talent than yeah u hav money bt u aint talented ….
To say something like insulting words in the song is stupidity, a matured thing can’t do something like that to be honest,,, anyway coz malawian musicians they’re full of kak
I never knew you are such a fool.Don’t you know that you can wake up tomorrow morning only to find out that you Mum is no longer a minister. Idiot