Tay Grin abweza moto

Advertisement
Tay Grin-Chipapa

Mfumu ya zinyau Limbani Kalilani imene imatchuka ndi dzina lodyera loti Tay Grin yakwera pa chulu ndikunena mokweza kuti anthu abalankhula chifukwa za iyo zinayera kale.

Tay Grin ndiotchuka pa mayimbidwe mu zamba zosiyanasiyana, choncho wagwiritsa ntchito luso lake pouza anthu onse akuthwa pakamwa kuti abayankhula, iyeyo sizikumukhuza. Kudzera mu mayimbidwe ake a tsopano otchedwa Lubwa, Kalilani wanena izi.

Tay Grin-Chipapa
Tay Grin watulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa ‘Lubwa’.

Nyimboyo yatuluka patapita masiku ochepa Grin atapambana zikho ziwiri mu Nyasa Music Awards. Iyeyu wanena zinthu zomwe anthu amamunena.

Zina zomwe wanena ndi zoti amake ndi nduna, iyeyo amakwera ndege kawirikawiri, komanso amatchena modetsa nkhawa. Izi sizinasangalase anthu ena pamene anena kuti katswiriyu wadzolera mafuta pa gulu.

“Ndkhumudwa naye koopsa Tay Grin. Zoona azikazitukumula?” Wafusa motero Angali Banda wa Ku Lilongwe

Tay Grin wakhala akutchuka ndi mbiri yoti samayankha anthu akamena zoipa za iyeyo. Koma apa zasonyeza kuti waatopera anthu onse amene akhala akumunena zinthu zosiyanasiyana.

Lubwa yayimbidwa mu chamba cha Ku South Africa chotchedwa house koma sanaiwale kuitendera ndi ng’oma yakwathu kuno. Anthu ena akondwera ndi mayimbidwe amenewa.

“Mkuluyu waonesa luso loti amatha kulowa palipose,” watero Grace Aleck wa ku Lilongwe.