Kwavuta ku University of Malawi

Advertisement

Kuli mfuwu ochuluka ku sukulu ya Ukachenjede ya Malawi pomwe bungwe lobwereketsa ngongole kwa ophunzira a m’ma sukulu a Ukachenjede alamura ena mwa ophunzira kumeneku kuti abwenze ma K175 000 omwe analowa kawiri.

Sabata yatha, kudali kuvina, kumwa, kumwemwetera pomwe ophunzirawa adalandira K350 000 yomwe ndi ya chaka m’malo mwa K175 000 ya semisita imodzi.

Ophunzirawa, omwe ambiri ndi ya chaka chachiwiri, sadafunse nzeru kapena kudekha atalandira ndalamayi, ndipo m’malo mwake, kunali kumwelera kuti ‘laponda la mphawi’.

M’tsogoleri wa ophunzirawa Thanx Elia Mwalwanda adawachenjezeratu anzakewa powauza kuti nkutheka osadzalandira ndalamayi mu semisita yachiwiri koma kunali koyenera kuti ayisamale ponena kuti bungweli ndi lomwe lidzapereke chiganizo chomaliza pa nkhaniyi.

Komatu zonsezi zinapita pachabe ndipo ophunzira ambiri omwe analandira kawiri, ndalamayi ayisosola yonse ndipo agwidwa njakata pomwe bungwe lobwereketsa ngongoleyi lawauza kuti ndalamayi ibwenzedwe pasanadutse pa 31 March yomwe ndi Lamulungu likudzari.

Bungweli lati akulu akulu oyendetsa sukuluyi avomera kuthandizira kuti ndalamayi ibwenzedwe kudzera ku ma account a padera a ophunzira aliyense amene analandira kawiri.

Komatu chiganizochi chawatulutsa thukuta ophunzirawa pomwe ambiri abwera poyera ndi ku ulura kuti anadya yonse.

Ma comment awo pa nkhaniyi, zaonetseratu kuti ndi ochepa omwe asamala ndalamayi ndipo sizikudziwika ngati ndalamayi ibwenzedwe pasanadutse pa 31.

Poyankhapo, a Mwalwanda ati ophunzira anzakewa asamuloze zala kamba kakuti adawachenjeza ndipo kunali koyenera kusamala podikira chiganizo kuchokera ku bungwe lobwereketsa ngongoleyi.

Tikunena pano, kwavuta ndi ku Unima, ophunzira ambiri mitu yayima.

Advertisement