Anthu ku Mzimba alembera chibaluwa phungu wawo

Advertisement
Jacob Hara

Anthu okhudzidwa ochokera ku dera la Solola m’boma la Mzimba alembera kalata ofesi ya mkulu wa boma ku khonsolo ya M’mbelwa kuti awapatse tsatanetsanane wa momwe ndalama za thumba la aphungu (CDF) m’mene zidagwilira ntchito m’derali zaka zingapo zapitazi. 

M’kalata yomwe yasayinidwa ndi mtsogoleri wawo, Geoffrey Lavedge Nyirenda, yomwe yapita kwa bwana Mkubwa wa bomali, komanso kwa phungu wa delari Jacob Hara, iwo ati pali kusowekera pochita zinthu poyera pakugwiritsa ntchito chuma chathumba la CDF m’derali. 

A Nyirenda ati zomwe akufuna kuti adziwe zambiri komanso kufotokoza za ndalama zomwe zidaperekedwa ndikugwiritsidwa ntchito pokwaniritsa ntchito zomwe zili pansi pa CDF mogwirizana ndi lamulo la kapezedwe ka mauthenga. 

Koma bwanamkubwa wa bomali Rodney Simwaka, watsimikiza za kulandira kalatayo, komanso ati khonsoloyo imatulutsa malipoti a momwe ndalama zimagwiritsidwira ntchito, zomwe ati munthu aliyense wokhudzidwa angathe kuzipeza kudzera mu njira zoyenera. 

Simwaka adalimbikitsa anthu okhudzidwawo kuti awerenge malipoti omwe adagawana ndi aphungu awo ndi makhansala ndipo apewe kugwiritsa ntchito maganizo mmalo mwa umboni pofunsa zambiri.

A Hara akana kuyikapo mulomo ponena kuti iwo sagwira ndalama za thumba la CDF.

Advertisement

One Comment

  1. Most of the time at all side is facing like this issues why . My complaint too to the minister of

Comments are closed.