Khanda lapsera m’nyumba mai ake atapita kokathyoletsa khobwe

Advertisement
Malawi24.com

Khanda la miyezi isanu ndi iwiri, lafa pomwe nyumba yomwe linagonekedwamo usiku lokhalokha inayaka moto pa nthawi yomwe mai ake anapita kokachita zadama ku nyumba kwa njonda ina.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi wofalitsa nkhani pa polisi ya boma la Kasungu a Joseph Kachikho omwe azindikira khandali ngati Ethel Petuli pomwe mai ake azindikilidwa ngati Mtisunge.

A Kachikho ati lolemba lapitali usiku, Mtisunge anatsekera mwana wakeyu m’nyumba yomwe amakhalamo m’mudzi wa a Chitsulo, mfumu yaikulu Chilowamatambe, m’boma la Kasungu kenaka iye ndikuwuyatsa ulendo wa ku nyumba kwa mdala wina yemwe amafuna kukasangalatsana naye.

Apolisi ati pakati pa usiku anthu omwe ayandikana ndi nyumba ya maiyu anangowona moto ukulilima pa denga la nyumba ya Mtisunge ndipo anthuwa anadzutsana ndikuyamba kuthimitsa motowo koma akuti anali odabwa kuti maiyo pa nthawi iyi samaoneka.

“Usiku umenewu, anthu oyandikana nawo nyumba anadzuka ndikuyamba kuzimitsa motowo koma adadziwa mochedwa kuti motowo udali utatentha kale khandalo mpaka kufa, koma anthuwa adadabwitsika kuona kuti pamene izi zimatichitika n’kuti mayiyu palibe, ndipo m’malo mwake adaonekera kum’mawa watsiku lotsatiralo,” adatero a Kachikho. 

Malingana ndi a Kachikho, zotsatira zachipatala chaching’ono  cha Chambwe zatsimikiza kuti mwanayu wafa kamba ka mabala amoto koma wati pakadali pano kafukufuku ali mkati kuti apeze chimene chinayambitsa moto umenewu.

Advertisement