A Akimu Phiri, m’modzi wa akatswiri ku nthambi yoona za nyengo m’dziko lino, achenjeza anthu omwe ndi atali atali kuti akuyenera kumayenda mosamala maka munyengo ya mvula ponena akuti anthuwa amakhala pa chiopsezo chowombedwa ndi mphenzi.
A Phiri anati anthu omwe ndi atali atali amakhala pa chiopsezo akamayenda pa malo oti palibe mitengo kapena zinthu zina zazitali kamba kakuti ziphaliwali zimakonda kutsikira pa zinthu zomwe zikuoneka zotalikirapo.
“Ukakhala kuti ukuyenda pa malo pomwe palibe chithu china chachitali pamene iwe uli wamtali, ndi kofunika kwambiri kuti chiphaliwali chikawomba uzigona pansi,” anatero a Phiri poyankhulana ndi wayilesa ya Kasungu.
Katswiriyu anapitiliza kuchenjeza anthu kuti azisamala malo okhala maka munyengo ya mvula kamba kakuti chiphaliwali chimakhala ndi nyesi yochuluka kwambili pafupifupi madigilizi 30,000.
Malingana ndi wayilesi ya Kasungu, a Phiri amayankhula m’boma la Mchinji pamaphunziro amasiku atatu omwe anakonzedwa ndi a Total Land Care okhudza za nyengo.
Wolemba: Vincent Madalitso Chauma (Kasungu Community Radio) ndi Ben Bongololo Gondwe