Monga muja tinalembera cha ku m’mawaku kuti m’tsogoleri wa chipani cha UTM a Michael Usi sakapikisana nawo ku convention ya UTM, iwo atsimikizadi masana ano kuti sakupanga nawo convention yi chifukwa kwachuluka phada.
Usi akuti sanatenge zikalata zowonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo ndipo sakapezekaso ku mkumanowu.
Mwazina a Usi akuti sakufuna kutenga nawo gawo pa zomwe apanga a kulu akulu ena a UTM zosatsata malamulo.