Oyimba yemwe ali m’dziko la America Alberto Fernando Zacharias yemwe amadziwika ndi dzina loti Jolly Bro mwachidule JB, wayankha za galimoto yomwe Tay Grin wapatsidwa ponena kuti iye samadalira zinthu zopatsidwa.
Izi zikudza kutsatira zomwe yachita imodzi mwa makampani obwereketsa magalimoto mdziko muno ya Diplomats Car Hire yomwe lachitatu sabata yatha yapereka galimoto yatsopano ya mtundu wa Nissan Patrol V8 kwa woyimba Tay Grin.
Akuluakulu a kampaniyi ati apeleka mphotoyi kwa Tay Grin yemweso amadziwika ndi dzina loti Nyau King chifukwa cha chidwi chake cholimbikitsa nkhondo yolimbana ndi kubedwa kwa anthu akhungu la chi alubino kudzera mu kanema wa ‘Misnomer’.
Nkhaniyi itadziwika, anthu ambiri m’masamba a nchezo anamukodola JB kuti ayikilepo mlomo za mphatsoyi potengera kuti awiriwa zimaonetsa kuti ali pa udani wa khoswe ndi mphaka ndipo zilumika zingapo zadutsa awiriwa osamwerana madzi.
Ndipo poyankha kudzera pa tsamba lake la fesibuku, Jolly Bro yemwe anatchuka pakatipa kaamba kong’alura oyimba anzake mdziko muno, anati iye amazilimbikilira yekha kugobola kuti apeze zokhumba mtima wake.
Mu kanema wake yemwe anatulutsa komaso zomwe wakhala akulemba pa tsamba lake fesibuku kwa masiku angapo, JB wati sikuti iye angachite dumbo kuti ‘Mfumu ya Zinyau’ yapatsidwa galimoto ya pamwambayo.
Iye anati palibe chifukwa chochitira kaduka ponena kuti iye akukhala moyo wapamwamba mdziko la America komaso kuti ali ndi chilichose chofunika m’moyo kuphatikizapo galimoto yomwe akuti anaipeza atakhetsa thukuta osati kuchita kupatsidwa.
“JB sakusowekera kuthandizidwa, amazithandiza yekha. Ife zopatsidwa ayi, ndalama timapanga tokha, ndife mafana amu sitiliti (street) America ndaikhala nthawi yaitali, nde wina asamaone ngati achina JB amadalira wina wake, mayazi. Timadana ndizoti anthu azinena kuti atilemeretsa ndi iwowo.
“Nde kaya muzipatsana zinthu zisamandikhudze ine, ine ndimadalira Mulungu ndiamene amandipatsa chuma changa. Ndayankha chifukwa ndawona anthu ambiri akundilemba pa fesibuku kuti a JB ndekuti akupanga nsanje, ine sindingapange nsanje chifukwa siine ozuzika. Musamaone ngati mukamagulirana ma Vitz zizindipweteka. Zindipweteka bwanji pamene chili chonse ndili nacho, galimoto ili panjapo. Kaya apatsana ma galimoto ine sizikundikhudza, ndipo musandiikemo munkhani iimeneyo,” anatelo JB mu kanema wake la chinayi.
Mumauthenga ake ena omwe analemba pa fesibuku, Jolly Bro wati podziwa kuti sikadza kokha kaopa kulawura, anthu akuyenera azithamanga thamanga kuti azizipangira okha chuma ponena kuti zopatsidwa kutukwanitsa komaso wati ukapatsidwa chinthu umakhala kapolo kwa okupatsayo.
“Palibe chidule m’moyo. Palibe chinthu chaulele, nthawi zonse pamakhala ka mtengo kena kake kobisika. Osamangoti manja lobodo apa, kumatchukuma,” watelo JB m’mauthenga ake angapo pa fesibuku.
Pofuna kutsindika kuti iye ndi khumutcha, JB wati posachedwapa m’mwezi wa September chaka chino apangitsa phwando la mayimbidwe ku America komko yiwme wati ndi mbali imodzi yokondwelera kuti wakwanitsa zaka makumi anayi (40).